Salimo 25:1-22
Salimo la Davide.
א [ʼAʹleph]
25 Ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova.+
ב [Behth]
2 Inu Mulungu wanga, chikhulupiriro changa chili mwa inu.+Musalole kuti ndichite manyazi.Adani anga asakondwere chifukwa cha masautso anga.+
ג [Giʹmel]
3 Ndithudi, palibe aliyense amene adzachita manyazi mwa anthu amene chiyembekezo chawo chili mwa inu.+Amene adzachite manyazi ndi amene akuchita zinthu mwachinyengo koma osaphula kanthu.+
ד [Daʹleth]
4 Ndidziwitseni njira zanu, inu Yehova.+Ndiphunzitseni kuyenda m’njira zanu.+
ה [Heʼ]
5 Ndiyendetseni m’choonadi chanu ndi kundiphunzitsa,+Pakuti inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.+
ו [Waw]Chiyembekezo changa chili mwa inu tsiku lonse.+
ז [Zaʹyin]
6 Kumbukirani chifundo chanu,+ inu Yehova, ndi zochita zanu zosonyeza kukoma mtima kosatha.+Pakuti munayamba kuchita zimenezo kale kwambiri.+
ח [Chehth]
7 Musakumbukire machimo a pa unyamata wanga ndi zolakwa zanga.+Ndikumbukireni malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha,+Ndiponso chifukwa cha ubwino wanu, inu Yehova.+
ט [Tehth]
8 Yehova ndi wabwino ndi wolungama.+N’chifukwa chake amalangiza ochimwa kuti ayende m’njira yoyenera.+
י [Yohdh]
9 Adzachititsa ofatsa kutsatira zigamulo zake,+Ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuyenda m’njira yake.+
כ [Kaph]
10 M’njira zonse za Yehova muli kukoma mtima kosatha ndi choonadiKwa anthu osunga pangano+ lake ndi zikumbutso zake.+
ל [Laʹmedh]
11 Chifukwa cha dzina lanu, inu Yehova,+Mundikhululukire cholakwa changa ngakhale kuti n’chachikulu.+
מ [Mem]
12 Tsopano munthu woopa Yehova ndani?+Adzamulangiza kuyenda m’njira imene adzasankha.+
נ [Nun]
13 Moyo wake udzasangalala ndi ubwino wa Mulungu,+Mbadwa zake zidzatenga dziko lapansi kukhala lawo.+
ס [Saʹmekh]
14 Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa,+Pangano lakenso ndi la anthu oterowo, ndipo iye amawadziwitsa panganolo.+
ע [ʽAʹyin]
15 Maso anga amayang’ana kwa Yehova nthawi zonse,+Chifukwa iye ndi amene amawonjola phazi langa mu ukonde.+
פ [Peʼ]
16 Ndicheukireni ndi kundikomera mtima.+Pakuti ndasungulumwa ndipo ndasautsika.+
צ [Tsa·dheh]
17 Masautso a mtima wanga awonjezeka.+Ndilanditseni ku nkhawa zimene zili pa ine.+
ר [Rehsh]
18 Onani masautso anga ndi mavuto anga,+Ndipo mundichotsere machimo anga onse.+
19 Onani mmene adani anga achulukira,+Ndipo chifukwa cha chidani chawo chachikulu, amafuna kundichitira chiwawa.+
ש [Shin]
20 Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa.+Musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndathawira kwa inu.+
ת [Taw]
21 Mtima wanga wosagawanika ndiponso wowongoka unditeteze,+Pakuti chiyembekezo changa chili mwa inu.+
22 Inu Mulungu, wombolani Isiraeli m’masautso ake onse.+