Salimo 120:1-7
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
120 Ndinafuulira Yehova m’masautso anga,+Ndipo iye anandiyankha.+
2 Inu Yehova, ndilanditseni ku milomo yonama,+Ndi ku lilime lachinyengo.+
3 Kodi iwe lilime lachinyengo,+Munthu adzakupatsa chiyani ndipo adzawonjezera chiyani pa iwe?
4 Adzakupatsa mivi yakuthwa ya munthu wamphamvu,+Pamodzi ndi makala amoto a mtengo wa m’chipululu.+
5 Tsoka kwa ine! Chifukwa ndakhala mlendo m’dziko la Meseke.+Ndakhala muhema pakati pa mahema a Kedara.+
6 Ndakhala mumsasa nthawi yaitali+Pamodzi ndi anthu odana ndi mtendere.+
7 Ndimalimbikitsa mtendere,+ koma ndikalankhula,Iwo amafuna nkhondo.+