Salimo 16:1-11

Mikitamu* ya Davide. 16  Ndisungeni, inu Mulungu, pakuti ndathawira kwa inu.+   Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Yehova. Ubwino wanga sungakupindulitseni,+   Koma ungapindulitse oyera amene ali padziko lapansi.Anthu aulemerero amenewo, ndi amene ndimakondwera nawo.”+   Zopweteka zimachuluka kwa anthu amene amati akaona mulungu wina, amamuthamangira.+Ine sindidzatsanula nsembe zawo zachakumwa zothira magazi,+Ndipo sindidzatchula dzina lawo ndi milomo yanga.+   Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa,+ komanso chikho changa.+Inu mukundisungira bwino kwambiri cholowa changa.   Zingwe zoyezera zandigwera m’malo abwino.+Ndithudi, gawo limene ndapatsidwa ndalivomereza.   Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo.+Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera.+   Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.+Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.+   Choncho moyo wanga ukukondwera, ndipo ndidzakhala wosangalala.+Komanso ndidzakhala wotetezeka.+ 10  Pakuti simudzasiya moyo wanga m’Manda.+Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.+ 11  Mudzandidziwitsa njira ya moyo.+Chifukwa cha nkhope yanu, munthu adzakondwera mokwanira.+Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe mpaka muyaya.+

Mawu a M'munsi

“Mikitamu” ndi mawu amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo, koma tanthauzo lake lenileni silikudziwika.