Salimo 99:1-9
99 Yehova wakhala mfumu.+ Mitundu ya anthu inthunthumire.+Iye wakhala pa akerubi.+ Ndipo dziko lapansi linjenjemere.+
2 Yehova wasonyeza mu Ziyoni kuti ndi wamkulu,+Ndipo ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+
3 Iwo atamande dzina lanu.+Dzina lanu ndi lalikulu, lochititsa mantha ndi loyera.+
4 Iye amakonda chilungamo ngati mmene mfumu yamphamvu imachitira.+Inu mwakhazikitsa kulungama.+Mwakhazikitsa chiweruzo ndi chilungamo pakati pa ana a Yakobo.+
5 Kwezani Yehova Mulungu wathu+ ndipo muweramireni pachopondapo mapazi ake.+Iye ndi woyera.+
6 Mose ndi Aroni anali pakati pa ansembe ake,+Samueli anali pakati pa anthu amene anali kuitana pa dzina lake.+Iwo anali kuitana Yehova, ndipo iye anali kuwayankha.+
7 Mulungu anapitiriza kulankhula nawo mumtambo woima njo ngati chipilala.+Iwo anasunga zikumbutso zake ndi malangizo amene anawapatsa.+
8 Inu Yehova Mulungu wathu munawayankha.+Kwa iwo munasonyeza kuti ndinu Mulungu wokhululuka,+Ndiponso wopereka chilango chifukwa cha zochita zawo zoipa.+
9 Kwezani Yehova Mulungu wathu,+Ndipo weramani paphiri lake loyera.+Pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.+