Salimo 91:1-16
91 Aliyense wokhala m’malo otetezeka+ a Wam’mwambamwamba+Adzakhala wosungika mumthunzi wa Wamphamvuyonse.+
2 Ndidzauza Yehova kuti: “Inu ndinu pothawirapo panga ndi malo anga achitetezo,+Mulungu wanga amene ndimamukhulupirira.”+
3 Pakuti iye adzakupulumutsa mumsampha wa wosaka mbalame,+Ndi ku mliri wobweretsa masautso.+
4 Adzakutchinjiriza ndi mapiko ake,+Udzathawira pansi pa mapiko ake.+Choonadi chake+ chidzakhala chishango chako+ chachikulu ndi malo ako achitetezo.
5 Usiku sudzaopa choopsa chilichonse,+Ndipo sudzaopanso muvi+ woponyedwa masana,
6 Sudzaopa mliri umene umayenda mu mdima,+Kapena chiwonongeko chimene chimachitika dzuwa lili paliwombo.+
7 Anthu 1,000 adzagwa pambali pako,Ndipo anthu 10,000 adzagwa kudzanja lako lamanja.Koma palibe zoterezi zimene zidzakuchitikira.+
8 Udzayang’ana ndi maso ako,+Ndipo udzaona anthu oipa akulandira chilango.+
9 Popeza wanena kuti: “Yehova ndiye pothawirapo panga,”+Wapanga Wam’mwambamwamba kukhala malo ako okhalamo.+
10 Palibe tsoka limene lidzakugwera,+Ndipo ngakhale mliri sudzayandikira hema wako.+
11 Pakuti adzalamula angelo ake za iwe,+Kuti akuteteze m’njira zako zonse.+
12 Iwo adzakunyamula m’manja mwawo,+Kuti phazi lako lisawombe mwala uliwonse.+
13 Udzapondaponda mkango wamphamvu ndi njoka ya mamba,+Ndipo udzapondaponda mkango wamphamvu kwambiri ndi chinjoka.+
14 Mulungu wanena kuti: “Popeza wasonyeza kuti amandikonda,+Inenso ndidzamupulumutsa.+Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa.+
15 Adzandiitana ndipo ndidzamuyankha.+Ndidzakhala naye m’nthawi ya masautso.+Ndidzamupulumutsa ndi kumupatsa ulemerero.+
16 Ndidzamukhutiritsa ndi masiku ambiri,+Ndipo ndidzamuonetsa chipulumutso changa.”+