Salimo 79:1-13

Nyimbo ya Asafu. 79  Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa m’dziko limene ndilo cholowa chanu.+Aipitsa kachisi wanu woyera.+Awononga Yerusalemu ndi kumusandutsa bwinja.+   Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawo.+Matupi a okhulupirika anu awapereka kwa zilombo zakutchire.+   Atsanula magazi awo ngati madziKuzungulira Yerusalemu yense, ndipo palibe wowaika m’manda.+   Anthu oyandikana nafe akutitonza,+Anthu otizungulira akutinyoza ndi kutiseka.+   Haa! Inu Yehova, mukhala wokwiya mpaka liti? Kwamuyaya?+Kodi mkwiyo wanu udzakhala ukuyaka ngati moto mpaka liti?+   Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu amene akukunyalanyazani,+Ndi pa maufumu amene sakuitana pa dzina lanu.+   Pakuti iwo awononga mbadwa zonse za Yakobo,+Ndipo malo ake okhalamo awasandutsa bwinja.+   Musatiimbe mlandu chifukwa cha zolakwa za makolo athu.+Fulumirani! Tisonyezeni chifundo chanu,+Chifukwa tasautsika koopsa.+   Tithandizeni inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+Kuti dzina lanu lilemekezedwe.+Tipulumutseni ndi kutikhululukira* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+ 10  Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti: “Mulungu wawo ali kuti?”+Pamene mukubwezera anthu a mitundu inawo chifukwa cha magazi a atumiki anu amene anakhetsedwa,+Ife tidzaone ndi maso athu.+ 11  Mverani kuusa moyo kwa mkaidi.+Anthu opita kukaphedwa muwateteze ndi dzanja lanu lamphamvu.+ 12  Bwezerani anthu oyandikana nafe mwa kuwatsanulira chitonzo pachifuwa pawo maulendo 7,+Inu Yehova, muwabwezere chitonzo chimene anachita pa inu.+ 13  Koma ife, anthu anu, nkhosa zimene mukuweta,+Tidzakuyamikani mpaka kalekale.Tidzakutamandani ku mibadwomibadwo.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kuphimba.”