Salimo 84:1-12
Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.
84 Inu Yehova wa makamu,+Ine ndimakondadi chihema chanu chachikulu!+
2 Ndimalakalaka mabwalo a Yehova ndipo ndafookeratu chifukwa cholakalaka mabwalowo.+Mtima wanga ndi thupi langa zikufuula mosangalala kwa Mulungu wamoyo.+
3 Inu Yehova wa makamu, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,Ngakhale mbalame zapeza malo okhala pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu.Namzeze* wadzimangira chisa chake pamenepo,Ndi kuikamo ana ake!
4 Odala ndi anthu amene akukhala m’nyumba yanu!+Iwo akupitirizabe kukutamandani.+ [Seʹlah.]
5 Odala ndi anthu amene amapeza mphamvu kuchokera kwa inu,+Amene mtima wawo umalakalaka misewu yaikulu yopita kunyumba yanu.+
6 Poyenda m’chigwa chouma mmene muli zitsamba za baka,*+Amasandutsa chigwacho kukhala choyenda madzi ochokera pakasupe,Mlangizi wafunda mawu otamanda.+
7 Mphamvu zawo zidzapitiriza kuwonjezeka pamene akuyenda.+Aliyense wa iwo amaonekera kwa Mulungu mu Ziyoni.+
8 Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa,+Tcherani khutu, inu Mulungu wa Yakobo.+ [Seʹlah.]
9 Inu Mulungu chishango chathu, onani,+Ndipo yang’anani nkhope ya wodzozedwa wanu.+
10 Pakuti kukhala tsiku limodzi m’mabwalo anu n’kwabwino kuposa kukhala masiku 1,000 kwina.+Ndasankha kuima pakhomo la nyumba ya Mulungu wanga+Kuposa kukhala m’mahema a anthu oipa.+
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa+ ndiponso chishango.+Iye amatikomera mtima ndi kutipatsa ulemerero.+Yehova samana anthu oyenda mosalakwa chinthu chilichonse chabwino.+
12 Inu Yehova wa makamu, wodala ndi munthu amene amakhulupirira inu.+
Mawu a M'munsi
^ Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”
^ Dzina lakuti “baka” ndi lochokera ku Chiheberi. Chitsamba chimenechi sichikudziwika kuti chinali chotani.