Salimo 10:1-18
ל [Laʹmedh]
10 N’chifukwa chiyani inu Yehova mukuima kutali?+N’chifukwa chiyani mukubisala pa nthawi ya masautso?+
2 Modzikweza, woipa amathamangitsa wosautsika,+Ndipo wosautsikayo amakodwa ndi maganizo amene woipa walingalira.+
3 Pakuti woipa amadzitamandira ndi zilakolako zake zadyera,+Ndipo wopanga phindu lachinyengo+ amadzitamanda.נ [Nun]Iye amanyoza Yehova.+
4 Chifukwa cha kutukumuka mtima kwake, woipa safufuza kuti adziwe Mulungu.+Iye amangoganiza kuti: “Kulibe Mulungu.”+
5 Zochita zake zimayenda bwino nthawi zonse.+Zigamulo zanu zili pamwamba kwambiri pamene iye sangathe kuziona.+Onse omuchitira zoipa amawanyodola.+
6 Mumtima mwake amanena kuti: “Sindidzagwedezeka.+Palibe chimene chidzandichitikira ku mibadwomibadwo.”+
פ [Peʼ]
7 M’kamwa mwake mwadzaza matemberero, chinyengo ndi kupondereza ena.+Pansi pa lilime lake pamatuluka mavuto ndi zopweteka ena.+
8 Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi.Amabisalira munthu wosalakwa ndi kumupha.+
ע [ʽAʹyin]Maso ake amafunafuna waumphawi.+
9 Amadikirira anthu pamalo obisika ngati mkango pamalo ake obisalapo.+Amawadikirira+ kuti atenge mokakamiza munthu wosautsika.Amakulunga wosautsika mu ukonde wake ndi kumutenga mokakamiza.+
10 Wosautsikayo amaponderezedwa, amawerama ndi chisoni,Ndipo khamu la anthu achisoni limagwera m’manja amphamvu a woipayo.+
11 Mumtima mwake+ amanena kuti: “Mulungu waiwala zochita zanga.+Wabisa nkhope yake.+Ndithudi, sadzaona kalikonse.”+
ק [Qohph]
12 Nyamukani,+ inu Yehova. Inu Mulungu, tukulani dzanja lanu.+Musaiwale anthu osautsika.+
13 N’chifukwa chiyani woipa amanyoza Mulungu?+Mumtima mwake amati: “Simudzandiimba mlandu.”+
ר [Rehsh]
14 Inu mwaona mavuto ndi masautso.Mumawayang’anabe kuti muchitepo kanthu.+Waumphawi,+ mwana wamasiye,* amadziikiza m’manja mwanu.Inu mwakhala mthandizi wake.+
ש [Shin]
15 Thyolani dzanja la woipa ndi wankhanzayo.+Fufuzani zoipa zake zonse ndi kumulanga kufikira zoipazo zitatha.+
16 Yehova ndi Mfumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+Mitundu yatheratu padziko lapansi.+
ת [Taw]
17 Mudzamva kuchonderera kwa anthu ofatsa,+ inu Yehova.Mudzakonzekeretsa mitima yawo.+Mudzatchera khutu lanu,+
18 Kuti muweruze mwana wamasiye komanso woponderezedwa.+Mudzatero kuti munthu wamba wochokera kufumbi asachititsenso anthu ena kunjenjemera.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”