Salimo 45:1-17
Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.* Salimo la ana a Kora. Masikili.* Nyimbo yonena za akazi okondedwa.
45 Mtima wanga wagalamuka chifukwa cha nkhani yosangalatsa.+Ine ndikuti: “Nyimbo yangayi ikunena za mfumu.”+Lilime langa likhale ngati cholembera+ cha wokopera malemba waluso.+
2 Ndiwedi wokongola kwambiri kuposa ana a anthu.+Mawu otuluka m’kamwa mwako ndi osangalatsadi.+N’chifukwa chake Mulungu adzakupatsa madalitso mpaka kalekale.+
3 Mangirira lupanga lako+ m’chiuno mwako wamphamvu iwe,+Limodzi ndi ulemu ndiponso ulemerero wako.+
4 Ndipo upambane mu ulemerero wako.+Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo,+Ndipo dzanja lako lamanja lidzakulangiza mu zinthu zochititsa mantha.+
5 Mivi yako yakuthwa idzalasa mitima ya adani a mfumu,+Mitundu ya anthu idzagwa pamapazi ako.+
6 Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo.+
7 Umakonda chilungamo+ ndipo umadana ndi zoipa.+N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako,+ wakudzoza+ ndi mafuta achikondwerero chachikulu+ kuposa cha mafumu ena.+
8 Zovala zako zonse ndi zonunkhira mafuta a mule, aloye ndi kasiya.*+Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera m’chinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.+
9 Ana aakazi+ a mafumu ali m’gulu la akazi ako okondedwa.Mkazi wamkulu wa mfumu+ waima kudzanja lako lamanja atavala zovala zagolide wa ku Ofiri.+
10 Iwe mwana wanga wamkazi, mvetsera ndipo ona ndi kutchera khutu.Uiwale anthu ako ndi nyumba ya bambo ako.+
11 Mfumu idzalakalaka kukongola kwako,+Pakuti ndiyo mbuye wako,+Choncho iweramire.+
12 Mwana wamkazi wa ku Turo alinso komweko ndi mphatso,+Olemera pakati pa anthu adzakhazika pansi mtima wako.+
13 Mwana wamkazi wa mfumu ali pa ulemerero waukulu m’nyumba ya mfumu.+Zovala zake ndi zagolide.
14 Adzamubweretsa kwa mfumu atavala chovala choluka.+Anamwali anzake omuperekeza akubwera nawo kwa iwe.+
15 Adzawabweretsa akusangalala ndi kukondwera.Ndipo adzalowa m’nyumba ya mfumu.
16 Ana anu adzatenga+ malo a makolo anu,+Ndipo mudzawaika kukhala akalonga padziko lonse lapansi.+
17 Ndidzatchula dzina lanu m’mibadwo yonse yam’tsogolo.+N’chifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.
Mawu a M'munsi
^ N’kutheka kuti “Maluwa” chinali chipangizo choimbira cha zingwe 6.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.