Salimo 38:1-22

Nyimbo ya Davide ya chikumbutso. 38  Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,+Kapena kundilanga mutapsa mtima.+   Pakuti mivi yanu yandilasa kwambiri,+Ndipo dzanja lanu likundilemera.+   Palibe pabwino m’thupi langa chifukwa cha chidzudzulo chanu.+Ndipo m’mafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.+   Pakuti zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga.+Zandilemera kwambiri ngati katundu wolemera.+   Zilonda zanga zanunkha ndi kunyeka,Chifukwa cha kupusa kwanga.+   Ndasokonezeka ndipo ndawerama kwambiri chifukwa cha chisoni changa.+Ndayenda uku ndi uku tsiku lonse ndili wachisoni.+   M’chiuno mwanga mukutentha kwambiri,Ndipo palibe paliponse pabwino m’thupi langa.+   Ndalefuka ndipo ndaponderezeka kwambiri.Ndikulira mofuula chifukwa cha kuvutika kwa mtima wanga.+   Inu Yehova, zokhumba zanga zonse zili pamaso panu,Kudandaula kwanga sikunabisike kwa inu.+ 10  Mtima wanga ukugunda kwambiri, ndipo mphamvu zanga zatha,Maso anga achita mdima.+ 11  Anthu amene anali kundikonda ndiponso anzanga aima patali chifukwa cha kuvutika kwanga,+Ndipo mabwenzi anga apamtima anditalikira.+ 12  Anthu amene akufuna kundiwononga anditchera misampha,+Amene akufuna kundivulaza akulankhula motsutsana nane,+Ndipo amakhala akukonza zachinyengo tsiku lonse.+ 13  Koma ine ndakhala ngati munthu wogontha, sindikumvetsera,+Ndakhala ngati munthu wosalankhula, sindikutsegula pakamwa.+ 14  Ndakhala ngati munthu wosamva,Sindikulankhula zotsutsana nawo. 15  Pakuti ine ndikuyembekezera inu Yehova.+Inu Yehova Mulungu wanga, mudzandiyankha.+ 16  Ine ndinati: “Ngati simundiyankha adani anga adzasangalala chifukwa cha kusautsika kwanga.+Phazi langa likaterereka,+ iwo adzadzikweza pamaso panga.”+ 17  Ndinali pafupi kupunthwa,+Ndipo ndinali kumva ululu nthawi zonse.+ 18  Pakuti ndinali kulankhula za cholakwa changa.+Ndipo ndinali kudera nkhawa za tchimo langa.+ 19  Adani anga anali amphamvu kwambiri,+Ndipo odana nane popanda chifukwa anachuluka.+ 20  Iwo anali kundibwezera choipa m’malo mwa chabwino,+Ndikamayesetsa kuchita chabwino anali kunditsutsa.+ 21  Inu Yehova, musandisiye.Inu Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.+ 22  Fulumirani kundithandiza,+Inu Yehova, chipulumutso changa.+

Mawu a M'munsi