Salimo 64:1-10
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
64 Inu Mulungu, imvani mawu ofotokoza nkhawa zanga.+Tetezani moyo wanga kuti usaope mdani.+
2 Ndibiseni kuti ndisamve zinsinsi za anthu ochita zoipa,+Kuti ndisamve phokoso la anthu ochita zovulaza anzawo,+
3 Amene anola lilime lawo ngati lupanga,+Amene alunjikitsa mivi yawo, imene ndi mawu awo owawa,+
4 Pa munthu wosalakwa, kuti amulase atamubisalira.+Amamulasa modzidzimutsa ndipo saopa.+
5 Amaumirira kulankhula zoipa,+Amakambirana kuti atchere misampha.+Iwo amati: “Angaione ndani?”+
6 Amafunafuna kuchita zinthu zosalungama,+Abisa chiwembu chimene achikonza mochenjera,+Ndipo zamkati, zamumtima mwa aliyense, n’zovuta kuzimvetsa.+
7 Koma Mulungu adzawalasa ndi muvi modzidzimutsa.+Iwo adzakhala ndi zilonda,+
8 Ndipo iwo amakhumudwitsa munthu,+Koma lilime lawo likutsutsana nawo.+Onse owayang’ana adzapukusa mitu yawo,+
9 Anthu onse adzachita mantha,+Ndipo adzanena za ntchito za Mulungu,+Iwo adzamvetsa bwino ntchito zake.+
10 Wolungama adzakondwera mwa Yehova ndipo adzathawira kwa iye,+Ndipo onse owongoka mtima adzatamanda Mulungu.+