Salimo 97:1-12

97  Yehova wakhala mfumu!+ Dziko lapansi likondwere,+Ndipo zilumba zambiri zisangalale.+   Mitambo ndi mdima wandiweyani zamuzungulira.+Chilungamo ndi chiweruzo ndizo malo okhazikika a mpando wake wachifumu.+   Patsogolo pake pakuyaka moto,+Ndipo ukupsereza adani ake onse omuzungulira.+   Mphezi zake zinawalitsa dziko lapansi.+Dziko linaona ndipo linachita mantha kwambiri.+   Mapiri anasungunuka ngati phula chifukwa cha Yehova,+Chifukwa cha Ambuye wa dziko lonse lapansi.+   Kumwamba kwalengeza za chilungamo chake,+Ndipo mitundu yonse ya anthu yaona ulemerero wake.+   Onse amene akupembedza chifaniziro chilichonse achite manyazi.+Amene amadzitama chifukwa cha milungu yopanda pake achite manyazi.+Muweramireni, inu milungu yonse.+   Ziyoni anamva ndipo anayamba kusangalala,+Midzi yozungulira Yuda inayamba kukondwera+Chifukwa cha zigamulo zanu, inu Yehova.+   Pakuti inu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba wolamulira dziko lonse lapansi.+Mwakwera pamwamba kwambiri kuposa milungu ina yonse.+ 10  Inu okonda Yehova+ danani nacho choipa.+Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika.+Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.+ 11  Kuwala kwaunikira wolungama,+Ndipo anthu owongoka mtima akusangalala.+ 12  Sangalalani chifukwa cha Yehova, anthu olungama inu,+Ndipo yamikirani dzina lake loyera.*+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chikumbutso chake choyera.”