Salimo 139:1-24
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.
139 Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.+
2 Inu mumadziwa ndikakhala pansi kapena ndikaimirira.+Mumadziwa maganizo anga muli kutali.+
3 Mumandidziwa bwino pamene ndikuyenda komanso pamene ndikugona,+Ndipo njira zanga zonse mukuzidziwa bwino.+
4 Ndisananene kanthu,+Inu Yehova mumakhala mutadziwa kale zonse.+
5 Mwandizungulira,Ndipo mwaika dzanja lanu pa ine.
6 Kwa ine ndi zovuta kwambiri kuti ndidziwe zinthu zonsezi.+Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+
7 Ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu,+Ndipo ndingapite kuti kuthawa nkhope yanu?+
8 Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko.+Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda, taonani! inunso mudzakhala komweko.+
9 Ngati ndingakwere pamapiko+ a m’bandakucha,Kuti ndikakhale m’nyanja ya kutali kwambiri,+
10 Kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera,+Dzanja lanu lamanja lidzandigwira.+
11 Ngati ndinganene kuti: “Ndithudi mdima undipeze mofulumira!”+Pamenepo mdima udzasanduka kuwala pa ine.+
12 Ndipo mdimawo sudzakhala mdima wandiweyani kwa inu,+Koma usiku udzakuwalirani ngati masana.+Mdima udzangokhala ngati kuwala.+
13 Inu munapanga impso zanga,+Ndipo munali kunditchinga m’mimba mwa mayi anga.+
14 Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.+Ntchito zanu ndi zodabwitsa,+Ndipo ine ndimadziwa bwino zimenezi.+
15 Mafupa anga sanali obisika kwa inu+Pamene munali kundipanga m’malo obisika,+Pamene munali kundiwomba ngati nsalu m’malo apansi kwambiri+ padziko lapansi.
16 Maso anu anandiona pamene ndinali mluza,+Ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa+Koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.
17 Choncho kwa ine maganizo anu ndi ofunika kwambiri,+ inu Mulungu,Ndipo ndi ochuluka zedi.+
18 Nditati ndiyese kuwawerenga, angakhale ochuluka kwambiri kuposa mchenga.+Podzuka ndingakhale ndikuwawerengabe.+
19 Inu Mulungu, zikanakhala bwino mukanapha woipa.+Pamenepo anthu amene ali ndi mlandu wa magazi+ akanandichokera,
20 Anthu amene amanena zam’mutu mwawo zotsutsana ndi inu.+Adani anuwo+ agwiritsa ntchito dzina lanu mosasamala.+
21 Inu Yehova, pajatu ine ndimadana ndi anthu amene amadana nanu kwambiri,+Ndipo anthu okupandukirani ndimanyansidwa nawo.+
22 Ndimadana nawo kwambiri.+Kwa ine akhala adani enieni.+
23 Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga.+Ndisanthuleni ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere,+
24 Ndipo muone ngati mwa ine muli chilichonse chimene chikundichititsa kuyenda m’njira yoipa,+Ndipo munditsogolere m’njira+ yamuyaya.