Salimo 116:1-19

116  Mtima wanga ndi wodzaza ndi chikondi, chifukwa Yehova amamva+Mawu anga ndi madandaulo anga.+   Pakuti watchera khutu lake kwa ine,+Ndipo ndidzaitanira pa iye masiku onse a moyo wanga.+   Zingwe za imfa zinandizungulira+Ndipo ndinasautsika ngati kuti ndili m’Manda.+Ndinapitiriza kusautsika ndi kukhala wachisoni,+   Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+“Inu Yehova, pulumutsani moyo wanga!”+   Yehova ndi wachisomo ndi wolungama.+Mulungu wathu amasonyeza chifundo.+   Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+Ndinali wosautsika koma iye anandipulumutsa.+   Iwe moyo wanga, bwerera kumalo ako ampumulo,+Pakuti Yehova wakuchitira zinthu zabwino.+   Pakuti inu mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,+Mwateteza maso anga kuti asakhetse misozi ndiponso phazi langa kuti lisapunthwe.+   Ndidzayenda+ pamaso pa Yehova m’dziko la anthu amoyo.+ 10  Ndinali ndi chikhulupiriro,+ n’chifukwa chake ndinalankhula.+Ndinali kusautsika kwambiri. 11  Pamene ndinapanikizika ndinati:+“Munthu aliyense ndi wabodza.”+ 12  Yehova ndidzamubwezera chiyani+Pa zabwino zonse zimene wandichitira?+ 13  Ndidzamwa za m’kapu yachipulumutso chachikulu,+Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+ 14  Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+Pamaso pa anthu ake onse. 15  M’maso mwa YehovaImfa ya anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu.+ 16  Inu Yehova,+Inetu ndine mtumiki wanu.+Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi.+Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+ 17  Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+ 18  Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+Ndidzawakwaniritsa pamaso pa anthu ake onse,+ 19  M’mabwalo a nyumba ya Yehova,+Pakati pa iwe Yerusalemu.+Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi