Salimo 146:1-10
146 Tamandani Ya, anthu inu!+Iwe moyo wanga, tamanda Yehova.+
2 Ndidzatamanda Yehova pamene ndili moyo.+Ndidzaimbira Mulungu wanga nyimbo zomutamanda kwa moyo wanga wonse.+
3 Musamakhulupirire anthu olemekezeka,+Kapena mwana wa munthu wina aliyense wochokera kufumbi amene alibe chipulumutso.+
4 Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+
5 Wodala ndi munthu amene thandizo lake limachokera kwa Mulungu wa Yakobo,+Amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake,+
6 Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,+Nyanja ndi zonse zili mmenemo.+Wosunga choonadi mpaka kalekale.+
7 Iye ndi Woperekera chiweruzo anthu ochitiridwa chinyengo,+Wopereka chakudya kwa anthu anjala.+Yehova amamasula anthu omangidwa.+
8 Yehova amatsegula maso a anthu akhungu.+Yehova amaweramutsa anthu owerama chifukwa cha masautso.+Yehova amakonda anthu olungama.+
9 Yehova amayang’anira alendo okhala m’dziko la eni.+Amathandiza mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.+Koma njira+ ya anthu oipa amaichititsa kukhala yovuta kuyendamo.+
10 Yehova adzakhala mfumu mpaka kalekale,+Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzakhala mfumu ku mibadwomibadwo.+Tamandani Ya, anthu inu!+