Salimo 89:1-52
Masikili.* Salimo la Etani wa m’banja la Zera.+
89 Ndidzaimba mpaka kalekale za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+Ndidzalengeza ndi pakamwa panga ku mibadwomibadwo za kukhulupirika kwanu.+
2 Pakuti ndanena kuti: “Kukoma mtima kwanu kosatha kudzakhazikika mpaka kalekale.+Ndipo mwakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba.”+
3 Mulungu anati: “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga.+Ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga,+
4 ‘Ndidzakhazikitsa mbewu yako mpaka kalekale,+Ndipo ndidzalimbitsa mpando wako wachifumu+ ku mibadwomibadwo.’” [Seʹlah.]
5 Inu Yehova, kumwamba kudzatamanda ntchito zanu zodabwitsa.+Mpingo wa oyera anu udzatamanda kukhulupirika kwanu.
6 Pakuti ndani kumwamba angayerekezeredwe ndi Yehova?+Ndani angafanane ndi Yehova pakati pa ana a Mulungu?+
7 Mulungu ayenera kuopedwa pakati pa gulu lake la oyera.+Iye ndi wamkulu ndi wochititsa mantha kuposa onse omuzungulira.+
8 Inu Yehova Mulungu wa makamu,+Ndani ali ndi mphamvu ngati inu Ya?+Ndinu wokhulupirika pa chilichonse.+
9 Nyanja ikadzaza mumailamulira.+Mafunde ake akamawinduka, inuyo mumawakhalitsa bata.+
10 Mwaphwanya Rahabi*+ ndi kumuchititsa kukhala ngati munthu amene waphedwa.+Mwabalalitsa adani anu ndi dzanja lanu lamphamvu.+
11 Kumwamba ndi kwanu,+ dziko lapansi nalonso ndi lanu.+Nthaka ya dziko lapansi ndiponso zinthu zimene zili mmenemo+ munazipanga ndinu.+
12 Munapanga kumpoto ndi kum’mwera.+Mapiri a Tabori+ ndi Herimoni+ amafuula mokondwera ndi kutamanda dzina lanu.+
13 Mkono wamphamvu ndi wanu,+Dzanja lanu ndi lamphamvu,+Dzanja lanu lamanja ndi lokwezeka.+
14 Chilungamo ndi chiweruzo ndizo maziko a mpando wanu wachifumu.+Kukoma mtima kosatha ndi choonadi zili pamaso panu.+
15 Odala ndi anthu amene amafuula mosangalala.+Iwo amayendabe m’kuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova.+
16 Iwo amakondwera ndi dzina lanu tsiku lonse.+Chilungamo chanu chimawakweza,+
17 Pakuti inu ndinu amene mumachititsa mphamvu zawo kukhala zaulemerero.+Ndipo mwa kukoma mtima kwanu, nyanga* yathu imakwezedwa.+
18 Pakuti chishango chathu ndi chochokera kwa Yehova,+Ndipo mfumu yathu ndi yochokera kwa Woyera wa Isiraeli.+
19 Pa nthawi imeneyo munalankhula ndi okhulupirika anu mwa masomphenya,+Ndipo munati:“Ndapereka thandizo kwa wamphamvu.+Ndakweza wosankhidwa mwapadera pakati pa anthu.+
20 Ndapeza Davide mtumiki wanga,+Ndipo ndamudzoza ndi mafuta anga opatulika.+
21 Dzanja langa lolimba lidzakhala pa iye.+Mkono wanga udzamulimbitsa.+
22 Palibe mdani amene adzamupondereza,+Ndipo palibe mwana aliyense wa anthu oipa amene adzamusautsa.+
23 Ndinaphwanya adani ake zidutswazidutswa ndi kuwachotsa pamaso pake,+Ndipo odana naye kwambiri ndinapitirizabe kuwamenya.+
24 Kukhulupirika kwanga ndi kukoma mtima kwanga kosatha kuli pa iye,+Ndipo nyanga yake imakwezedwa m’dzina langa.+
25 Ndinaika ulamuliro wake panyanja,+Ndipo ndinam’patsa ulamuliro pamitsinje.+
26 Iye amafuula kwa ine kuti, ‘Inu ndinu Atate wanga,+Mulungu wanga+ ndi Thanthwe la chipulumutso changa.’+
27 Inenso ndidzamuika kukhala mwana woyamba kubadwa,+Ndiponso mfumu yaikulu pa mafumu onse a padziko lapansi.+
28 Ndidzamusonyeza kukoma mtima kwanga kosatha mpaka kalekale,+Ndipo pangano limene ndinachita naye silidzaphwanyidwa.+
29 Ndidzakhazikitsa mbewu yake kwamuyaya,+Ndipo mpando wake wachifumu udzakhalapo kwa masiku ochuluka ngati masiku a kumwamba.+
30 Ana ake akadzasiya chilamulo changa,+Ndi kuleka kutsatira zigamulo zanga,+
31 Akadzanyoza mfundo zanga,Ndi kusasunga malamulo anga,
32 Ine ndidzawaimba mlandu ndi kuwalanga ndi ndodo,+Ndipo ndidzawalanga ndi zikoti chifukwa cha zolakwa zawo.+
33 Koma kukoma mtima kwanga kosatha sindidzakuchotsa pa iye,+Ndipo sindidzasiya kukhulupirika kwanga.+
34 Sindidzaphwanya pangano langa,+Ndipo sindidzasintha mawu otuluka pakamwa panga.+
35 Ndalumbira kamodzi kokha pa kuyera kwanga,+Davide sindidzamunamiza.+
36 Mbewu yake idzakhala mpaka kalekale,+Ndipo mpando wake wachifumu udzakhala ngati dzuwa pamaso panga.+
37 Udzakhazikika ngati mwezi mpaka kalekale,Udzakhala ngati mboni yokhulupirika ya m’mlengalengayo.” [Seʹlah.]
38 Koma inu mwataya wodzozedwa wanu moti mukupitiriza kunyansidwa naye,+Ndipo mwamukwiyira.+
39 Mwakana moipidwa pangano la mtumiki wanu.Mwanyoza chisoti chake chachifumu mwa kuchiponyera pansi.+
40 Mwagwetsa makola ake onse amiyala.+Mizinda yake yamipanda yolimba mwaisandutsa mabwinja.+
41 Onse oyenda njira imeneyo afunkha zinthu zake.+Iye wakhala chinthu chotonzedwa kwa anthu oyandikana naye.+
42 Mwakweza dzanja lamanja la adani ake.+Mwachititsa adani ake onse kusangalala.+
43 Kuwonjezera apo, mukuonanso lupanga lake ngati mdani,+Ndipo mwachititsa kuti iye asapambane pa nkhondo.+
44 Mwachititsa kuti kuwala kwake kuthe,+Mpando wake wachifumu mwauponyera pansi.+
45 Mwafupikitsa masiku a unyamata wake.Ndipo mwamukulunga ndi manyazi.+ [Seʹlah.]
46 Inu Yehova, kodi mudzadzibisa kufikira liti? Ku nthawi zonse?+Kodi mkwiyo wanu udzakhalabe ukuyaka ngati moto?+
47 Kumbukirani utali wa moyo wanga.+Kodi ana onse a anthu munawalenga pachabe?+
48 Kodi pali mwamuna wamphamvu aliyense amene sadzaona imfa?+Kodi angathe kupulumutsa moyo wake m’dzanja la Manda?+ [Seʹlah.]
49 Kodi zochita zanu zakale zija zosonyeza kukoma mtima kosatha zili kuti, inu Yehova?Zija zimene munalumbira kwa Davide chifukwa cha kukhulupirika kwanu?+
50 Inu Yehova, kumbukirani chitonzo chimene chagwera atumiki anu.+Kumbukirani kuti ndanyamula pachifuwa panga chitonzo cha mitundu yambiri ya anthu.+
51 Inu Yehova, kumbukirani mmene adani anu alankhulira motonza,+Mmene atonzera paliponse pamene mapazi a wodzozedwa wanu aponda.+
52 Adalitsike Yehova mpaka kalekale. Ame! Ame!*+
Mawu a M'munsi
^ Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo kapena Farao.
^ Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”