Salimo 134:1-3
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
134 Tamandani Yehova,+Inu nonse atumiki a Yehova,+Inu amene mumaimirira m’nyumba ya Yehova usiku.+
2 Pamene mukupemphera mutakweza manja anu, muzikhala oyera,+Ndipo tamandani Yehova.+
3 Yehova, amene ndiye Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,+Akudalitseni ali ku Ziyoni.+