Salimo 87:1-7

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. 87  Maziko a mzinda wa Mulungu ali m’mapiri opatulika.+   Yehova amakonda kwambiri zipata za Ziyoni+Kusiyana ndi mahema onse a Yakobo.+   Iwe mzinda wa Mulungu woona, anthu akunena za ulemerero wako.+ [Seʹlah.]   Ine ndidzatchula Rahabi*+ ndi Babulo+ monga ena mwa amene akundidziwa.Ponena za Filisitiya,+ Turo ndi Kusi ine ndidzati:“Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+   Ponena za Ziyoni anthu adzati:“Aliyense anabadwira mmenemo.”+Ndipo Wam’mwambamwamba+ adzakhazikitsa mzinda umenewo.+   Powerenga mitundu ya anthu, Yehova adzalengeza kuti:+“Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+ [Seʹlah.]   Kudzakhalanso oimba komanso ovina gule wovina mozungulira amene adzati:+“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”+

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo.