Salimo 58:1-11
Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.*
58 Kodi mungalankhule bwanji za chilungamo mutakhala chete?+Kodi mungaweruze molungama, inu ana a anthu?+
2 Ayi! Inu mukuchita zosalungama padziko lapansi mogwirizana ndi zimene mtima wanu ukufuna,+Ndipo mukukonza njira zochitira chiwawa ndi manja anu.+
3 Oipa akhala opotoka maganizo kuyambira ali m’mimba.+Iwo asochera kuyambira ali m’mimba,Ndipo amalankhula zabodza.+
4 Iwo ali ndi poizoni ngati wa njoka,+Ndipo ndi ogontha ngati njoka ya mamba imene yatseka makutu ake,+
5 Imene singamve mawu a munthu wamatsenga,+Ngakhale wina wanzeru ataimanga ndi mphamvu zamatsenga.+
6 Inu Mulungu, agululeni mano m’kamwa mwawo.+Inu Yehova, thyolani nsagwada za mkango wamphamvu.
7 Asungunuke ndi kupita ngati madzi.+Mulungu akunge uta woponyera mivi yake pamene adaniwo akugwa.+
8 Woipayo amayenda ngati nkhono imene ikusungunuka.Iwo sadzaona dzuwa ngati mwana wa mayi amene wapita padera.+
9 Miphika yanu isanayambe kumva kutentha kwa moto wa mitengo yaminga,+Mulungu adzauluza ndi mphepo yamkuntho mitengo yaiwisi yaminga pamodzi ndi imene ikuyaka.+
10 Wolungama adzasangalala chifukwa chakuti waona oipa akupatsidwa chilango.+Adzasambitsa mapazi ake m’magazi a anthu oipa.+
11 Ndipo mtundu wa anthu udzati:+ “Ndithudi wolungama adzalandira mphoto.+Ndithudi pali Mulungu amene akuweruza dziko lapansi.”+