Salimo 110:1-7

Salimo la Davide. 110  Yehova wauza Ambuye wanga kuti:+“Khala kudzanja langa lamanja+Kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”+   Yehova adzatambasula ndodo+ yako yachifumu yamphamvu kuchokera m’Ziyoni+ ndi kunena kuti:“Pita ukagonjetse anthu pakati pa adani ako.”+   Anthu ako+ adzadzipereka mofunitsitsa+ pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.+Wadzikongoletsa ndi ulemerero,+Ndipo gulu la achinyamata amene ali ngati mame a m’bandakucha lili pamodzi ndi iwe.+   Yehova walumbira+ (ndipo sadzasintha maganizo). Iye wati:+“Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,+Monga mwa unsembe wa Melekizedeki!”+   Yehova amene ali kudzanja lako lamanja+Adzaphwanyaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wake.+   Adzapereka chiweruzo pakati pa anthu a mitundu ina.+Adzachititsa mitembo ya anthu kupezeka paliponse.+Adzaphwanyaphwanya mtsogoleri wa dziko la anthu ambiri.+   Panjira, adzamwa madzi a m’chigwa.+N’chifukwa chake adzatukula kwambiri mutu wake.+

Mawu a M'munsi