Salimo 24:1-10
Salimo la Davide.
24 Dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi za Yehova,+Nthaka ndi yake pamodzi ndi onse okhala panthakapo.+
2 Iye anakhazika dziko lapansi molimba panyanja,+Ndipo analikhazikitsa mwamphamvu pamitsinje.+
3 Ndani angakwere m’phiri la Yehova?+Ndipo ndani anganyamuke kukalowa m’malo ake opatulika?+
4 Aliyense wopanda mlandu m’manja mwake ndi woyera mumtima mwake,+Amene sanaone Moyo wanga ngati wopanda pake,+Kapena kulumbira mwachinyengo.+
5 Ameneyo adzalandira madalitso kuchokera kwa Yehova,+Adzalandira chilungamo kuchokera kwa Mulungu wa chipulumutso chake.+
6 Umenewo ndiwo m’badwo wa amene amafunafuna Mulungu,M’badwo wa anthu ofunafuna nkhope yanu, inu Mulungu wa Yakobo.+ [Seʹlah.]
7 “Tukulani mitu yanu, inu zipata,+Ndipo dzitukuleni, inu makomo akale lomwe,+Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!”+
8 “Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndani?”+“Ndi Yehova, wanyonga ndi wamphamvu,+Yehova wamphamvu mu nkhondo.”+
9 “Tukulani mitu yanu, inu zipata,+Tukulani mitu, inu makomo akale lomwe,Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!”+
10 “Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndani?”“Ndi Yehova wa makamu. Iye ndiye Mfumu yaulemerero.”+ [Seʹlah.]