Salimo 35:1-28

Salimo la Davide. 35  Weruzani mlandu wanga inu Yehova, motsutsana ndi adani anga.+Menyani nkhondo ndi kugonjetsa amene akumenyana ndi ine.+   Tengani chishango chaching’ono ndi chishango chachikulu,+Ndipo bwerani kuti mundithandize.+   Tengani mkondo ndi nkhwangwa ya pankhondo kuti mukumane ndi anthu amene akundilondalonda.+Uzani moyo wanga kuti: “Ine ndine chipulumutso chako.”+   Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi ndi kunyozeka.+Amene akundikonzera chiwembu muwabweze ndipo athedwe nzeru.+   Akhale ngati mankhusu ouluzika ndi mphepo,+Mngelo wa Yehova awapitikitse.+   Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera,+Ndipo mngelo wa Yehova aziwathamangitsa.   Iwo andikumbira mbuna popanda chifukwa ndi kuikapo ukonde,+Akumba mbunazo kuti ndigweremo ngakhale kuti sindinalakwe.+   Awonongeke pamene iwo sakuyembekezera,+Akodwe mu ukonde umene atchera okha.+Agweremo ndi kuwonongeka.+   Koma moyo wanga ukondwere mwa Yehova.+Usangalale chifukwa cha chipulumutso chake.+ 10  Ndinene ndi mtima wanga wonse kuti:+“Inu Yehova, ndani angafanane ndi inu,+Amene mumalanditsa wosautsika m’manja mwa munthu wamphamvu kuposa iyeyo,+Amene mumalanditsa wozunzika ndi wosauka m’manja mwa munthu amene akumulanda zinthu zake?”+ 11  Mboni zachiwawa zimaimirira.+Zimandifunsa zinthu zimene sindikudziwa.+ 12  Adani anga amandibwezera zoipa m’malo mwa zabwino,+Ndipo ndimakhala wachisoni ngati wofedwa.+ 13  Iwo akadwala ndinali kuvala chiguduli,+Ndinali kusautsa moyo wanga mwa kusala kudya.+Ndipo mapemphero anga anali kubwerera kwa ine osayankhidwa.+ 14  Chifukwa cha mnzanga ndiponso m’bale wanga,+Ndinamva chisoni kwambiri ngati munthu wolira maliro a mayi ake.+Ndinawerama chifukwa cha chisoni. 15  Atandiona ndikuyenda motsimphina anasangalala ndipo anasonkhana pamodzi.+Anasonkhana pamodzi kuti alimbane nane.+Anandimenya pamene sindinali kuyembekezera.+Anandikhadzulakhadzula ndipo sanakhale chete.+ 16  Anthu ampatuko amene anali kunditonza kuti apeze kachakudya,+Anandikukutira mano.+ 17  Inu Yehova, kodi mudzayang’anira zimenezi kufikira liti?+Ndipulumutseni kwa anthu ofuna kundiwononga,+Pulumutsani moyo wanga+ ku mikango yamphamvu. 18  Ndidzakutamandani mu mpingo waukulu.+Ndidzakutamandani pakati pa anthu ambiri.+ 19  Musalole kuti anthu amene amadana ndi ine popanda chifukwa akondwere ndi kusautsika kwanga.+Ndipo musalole kuti anthu amene amandida popanda chifukwa anditsinzinire diso.+ 20  Iwo salankhula mawu amtendere,+Koma amakonzera chiwembu anthu ofatsa a padziko lapansi,Kuti awachitire zachinyengo.+ 21  Amatsegula kwambiri pakamwa pawo kuti atsutsane nane.+Iwo amati: “Eya! Eya! Tadzionera tokha.”+ 22  Inu Yehova, mwaona zimenezi+ ndipo musakhale chete.+Musakhale patali ndi ine, inu Yehova.+ 23  Nyamukani ndi kukhala maso kuti mundichitire chilungamo,+Chitani zimenezi inu Mulungu wanga Yehova, kuti muweruze mlandu wanga.+ 24  Inu Yehova Mulungu wanga, mundiweruze mogwirizana ndi chilungamo chanu,+Musalole kuti adani anga akondwere ndi kusautsika kwanga.+ 25  Musalole kuti mumtima mwawo anene kuti: “Eya! Izi ndi zimene timafuna.”+Ndipo asanene kuti: “Tamumeza.”+ 26  Onse amene akukondwera ndi tsoka langa,+Achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+Onse odzikweza pamaso panga achite manyazi+ ndi kutsitsidwa.+ 27  Onse amene amakonda chilungamo changa afuule mosangalala ndi kukondwera.+Nthawi zonse azinena kuti:+“Alemekezeke Yehova, amene amasangalala mtumiki wake akakhala pa mtendere.”+ 28  Lilime langa linene chapansipansi za chilungamo chanu,+Ndipo likutamandeni tsiku lonse.+

Mawu a M'munsi