Salimo 61:1-8
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe. Salimo la Davide.
61 Inu Mulungu, imvani kulira kwanga kochonderera.+Mvetserani pemphero langa mwatcheru.+
2 Mtima wanga ukalefuka, ndidzafuulira inu, kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+Nditsogolereni ndi kundikweza pamwamba pa thanthwe lalitali kuposa msinkhu wanga.+
3 Pakuti inu mwakhala pothawirapo panga,+Nsanja yolimba pamaso pa mdani.+
4 Ndidzakhala mlendo m’chihema chanu mpaka kalekale.+Ndidzathawira m’malo obisalamo kunsi kwa mapiko anu.+ [Seʹlah.]
5 Pakuti inu Mulungu, mwamvetsera malonjezo anga.+Mwandipatsa cholowa chimene mwasungira anthu oopa dzina lanu.+
6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu.+Zaka zake zidzachuluka kufanana ndi mibadwo yambirimbiri.+
7 Mfumuyo idzakhala pamaso pa Mulungu mpaka kalekale.+Isonyezeni kukoma mtima kwanu kosatha ndi kuipatsa choonadi kuti zimenezi ziiteteze.+
8 Choncho ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu mpaka muyaya,+Kuti ndikwaniritse malonjezo anga tsiku ndi tsiku.+