Salimo 48:1-14

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ 48  Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+Mumzinda wa Mulungu wathu,+ m’phiri lake loyera.+   Phiri la Ziyoni limene lili m’dera lakutali la kumpoto,+Ndi lokongola chifukwa lili pamalo okwezeka ndi osangalatsa padziko lonse lapansi,+Mudzi wa Mfumu Yaikulu.+   Munsanja zokhalamo za m’mudzimo, Mulungu wadziwika kuti ndi malo okwezeka ndiponso achitetezo.+   Taonani! Mafumu anakumana atapangana,+Koma anangodutsa.+   Iwo anaona ndipo anadabwa.Anasokonezeka, moti anathawa mopanikizika kwambiri.+   Kumeneko iwo anayamba kunjenjemera,+Anamva zopweteka ngati za mkazi amene akubereka.+   Pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kum’mawa, munaswa zombo za ku Tarisi.+   Ife taona zimene Mulungu anachita monga mmene tinamvera,+Mumzinda wa Yehova wa makamu, mumzinda wa Mulungu wathu.+Mulungu adzakhazikitsa mzindawo mpaka kalekale.+ [Seʹlah.]   Inu Mulungu, ife talingalira mozama za kukoma mtima kwanu kosatha,+Tili mkati mwa kachisi wanu.+ 10  Inu Mulungu, mofanana ndi dzina lanu,+ kukutamandaniKwafika kumalire a dziko lapansi.Dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.+ 11  Phiri la Ziyoni+ likondwere,Midzi yozungulira Yuda isangalale+ chifukwa cha zigamulo zanu.+ 12  Gubani mozungulira Ziyoni, anthu inu, ndipo yendayendani mmenemo,+Werengani nsanja zake.+ 13  Ganizirani mofatsa za khoma lake lolimba.+Yenderani nsanja zake zokhalamo,Kuti mudzasimbire m’badwo wam’tsogolo.+ 14  Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+Iye adzatitsogolera kufikira imfa yathu.+

Mawu a M'munsi