Salimo 145:1-21
Nyimbo yotamanda Mulungu. Salimo la Davide.
א [ʼAʹleph]
145 Ndidzakukwezani, inu Mfumu ndi Mulungu wanga,+Ndipo ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
ב [Behth]
2 Ndidzakutamandani tsiku lonse.+Ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
ג [Giʹmel]
3 Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+Ndipo ukulu wake ndi wosasanthulika.+
ד [Daʹleth]
4 Anthu adzatamanda ntchito zanu ku mibadwomibadwo,+Ndipo adzasimba za zochita zanu zamphamvu.+
ה [Heʼ]
5 Ndidzasinkhasinkha za ulemerero wanu waukulu+Ndi nkhani zokhudza ntchito zanu zodabwitsa.+
ו [Waw]
6 Anthu adzanena za zochita zanu zamphamvu ndi zochititsa mantha.+Ndipo ine ndidzalengeza za ukulu wanu.+
ז [Zaʹyin]
7 Iwo adzalankhula mosefukira za kuchuluka kwa ubwino wanu,+Ndipo adzafuula mokondwera chifukwa cha chilungamo chanu.+
ח [Chehth]
8 Yehova ndi wachisomo ndi wachifundo,+Wosakwiya msanga ndi wosonyeza kukoma mtima kosatha komanso kwakukulu.+
ט [Tehth]
9 Yehova amakomera mtima aliyense,+Ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.+
י [Yohdh]
10 Ntchito zanu zonse zidzakutamandani, inu Yehova,+Ndipo okhulupirika anu adzakutamandani.+
כ [Kaph]
11 Iwo adzanena za ulemerero wa ufumu wanu.+Ndi kulankhula za mphamvu zanu,+
ל [Laʹmedh]
12 Kuti ana a anthu adziwe za ntchito zanu zamphamvu+Ndi kukula kwa ulemerero wa ufumu wanu.+
מ [Mem]
13 Ufumu wanu ndi ufumu umene udzakhalapobe mpaka kalekale.+Ulamuliro wanu udzakhalapobe ku mibadwo yonse.+
ס [Saʹmekh]
14 Yehova amachirikiza amene ali pafupi kugwa,+Ndipo amaweramutsa onse amene awerama chifukwa cha masautso.+
ע [ʽAʹyin]
15 Zolengedwa zonse zimayang’ana kwa inu mwachiyembekezo,+Ndipo mumazipatsa chakudya pa nyengo yake.+
פ [Peʼ]
16 Mumatambasula dzanja lanu+Ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.+
צ [Tsa·dhehʹ]
17 Yehova ndi wolungama m’njira zake zonse,+Ndipo ndi wokhulupirika m’ntchito zake zonse.+
ק [Qohph]
18 Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.+Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi,+
ר [Rehsh]
19 Ndipo anthu amene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo,+Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.+
ש [Shin]
20 Yehova amayang’anira onse omukonda,+Koma oipa onse adzawafafaniza.+
ת [Taw]
21 Pakamwa panga padzalankhula zotamanda Yehova,+Ndipo anthu onse atamande dzina lake loyera mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+