Salimo 130:1-8
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
130 Inu Yehova, pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu.+
2 Imvani mawu anga Yehova.+Makutu anu amve mawu anga ochonderera.+
3 Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa,+Ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?+
4 Inu mumakhululukiradi,+Kuti anthu akuopeni.+
5 Ndayembekezera thandizo lanu, inu Yehova. Moyo wanga wayembekezera thandizo lanu.+Ine ndayembekezera mawu anu.+
6 Ndayembekezera Yehova+Kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche,+Ndithu kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche.+
7 Isiraeli ayembekezere Yehova,+Pakuti Yehova amasonyeza kukoma mtima kosatha.+Iye ali ndi mphamvu zochuluka zowombolera anthu ake.+
8 Iye adzawombola Isiraeli ku zolakwa zake zonse.+