Salimo 123:1-4
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
123 Ndakweza maso anga kuyang’ana inu,+Kuyang’ana inu amene mukukhala kumwamba.+
2 Taonani! Monga mmene maso a atumiki amayang’anira dzanja la mbuye wawo,+Mmene maso a kapolo wamkazi amayang’anira dzanja la mbuye wake wamkazi,+Momwemonso, maso athu adzayang’ana kwa Yehova Mulungu wathu,+Kufikira atatikomera mtima.+
3 Tikomereni mtima, inu Yehova, tikomereni mtima,+Pakuti tanyozeka kwambiri.+
4 Moyo wathu wasautsika kwambiri chifukwa cha kunyoza kwa anthu amene akukhala mosatekeseka,+Ndiponso chifukwa cha kunyoza kwa anthu odzikuza.+