Salimo 9:1-20

Kwa wotsogolera nyimbo pa Mutilabeni.* Nyimbo ya Davide. א [ʼAʹleph] 9  Ndidzakutamandani inu Yehova ndi mtima wanga wonse.+Ndidzalengeza ntchito zanu zonse zodabwitsa.+   Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha inu,+Ndidzaimba nyimbo motsagana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda dzina lanu, inu Wam’mwambamwamba.+ ב [Behth]   Adani anga akabweranso,+Adzapunthwa ndi kuwonongeka pamaso panu,+   Chifukwa mwandiweruzira mlandu wanga ndi dandaulo langa.+Mwakhala pampando wachifumu ndipo mukuweruza mwachilungamo.+ ג [Giʹmel]   Mwadzudzula anthu a mitundu ina,+ mwawononga oipa.+Dzina lawo mwalifafaniza mpaka kalekale, mwalifafaniza mpaka muyaya.+   Kusakaza kwa mdani kwatheratu tsopano,+Mizinda imene mwaifafaniza, nayonso yatheratu.+Dzina la mdani wanu silidzatchulidwanso.+ ה [Heʼ]   Koma Yehova adzakhala pampando wachifumu mpaka kalekale,+Adzakhazikitsa mpando wake wachifumu kuti aweruze.+   Iye adzaweruza anthu padziko lapansi mwachilungamo.+Adzazenga mlandu mitundu ya anthu moyenerera.+ ו [Waw]   Yehova adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo kwa aliyense woponderezedwa,+Adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo m’nthawi za masautso.+ 10  Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani,+Pakuti simudzasiya ndithu anthu okufunafunani, inu Yehova.+ ז [Zaʹyin] 11  Anthu inu, imbani nyimbo motsagana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda Yehova amene akukhala m’Ziyoni.+Fotokozani ntchito zake kwa mitundu ya anthu.+ 12  Pofunafuna okhetsa magazi,+ iye adzakumbukira ndithu anthu osautsidwa.+Sadzaiwala ndithu kulira kwawo.+ ח [Chehth] 13  Ndikomereni mtima inu Yehova. Onani mmene anthu odana nane akundisautsira,+Inu Mulungu amene mukundinyamula kundichotsa pazipata za imfa.+ 14  Ndichitireni zimenezi kuti ndilengeze ntchito zanu zonse zotamandika+Pazipata+ za mwana wamkazi wa Ziyoni,+Kuti ndikondwere ndi chipulumutso chanu.+ ט [Tehth] 15  Anthu a mitundu ina agwera m’dzenje limene anakumba okha.+Phazi lawo lakodwa mu ukonde+ umene anatchera okha.+ 16  Yehova amadziwika ndi ziweruzo zimene amapereka.+Woipa wakodwa mumsampha wa ntchito ya manja ake.+Higayoni.* [Seʹlah.] י [Yohdh] 17  Anthu oipa+ adzapita ku Manda,+Ngakhalenso anthu onse a mitundu ina amene aiwala Mulungu.+ 18  Pakuti waumphawi sadzaiwalidwa nthawi zonse,+Ndiponso chiyembekezo cha ofatsa sichidzatha konse.+ כ [Kaph] 19  Nyamukani, inu Yehova! Munthu asakuposeni mphamvu.+Anthu a mitundu ina aweruzidwe pamaso panu.+ 20  Ikani mantha m’mitima yawo, inu Yehova,+Kuti anthu a mitundu ina adziwe kuti iwo ndi anthu ochokera kufumbi.+ [Seʹlah.]

Mawu a M'munsi

“Mutilabeni” ndi mawu achiheberi amene tanthauzo lake lenileni silikudziwika. Koma omasulira ena anamasulira mawuwa kuti, “yonena za imfa ya mwana wamwamuna.”
“Higayoni” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo, koma tanthauzo lake lenileni silikudziwika.