Salimo 128:1-6
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
128 Wodala ndi aliyense woopa Yehova,+Amene amayenda m’njira za Mulungu.+
2 Pakuti udzadya zipatso za ntchito ya manja ako.+Udzakhala wodala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+
3 Mkazi wako adzakhala ngati mtengo wa mpesa wobala zipatso+Mkati mwa nyumba yako.Ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya maolivi+ kuzungulira tebulo lako.
4 Taonani! Mwamuna aliyense wamphamvu woopa Yehova+Adzadalitsidwa mwa njira imeneyi.+
5 Yehova adzakudalitsa ali ku Ziyoni.+Komanso usangalale ndi zinthu zabwino za mu Yerusalemu masiku onse a moyo wako,+
6 Ndipo uone ana a ana ako.+Mtendere ukhale pa Isiraeli.+