Salimo 15:1-5
Nyimbo ya Davide.
15 Inu Yehova, ndani amene angakhale mlendo m’chihema chanu?+Ndani angakhale m’phiri lanu lopatulika?+
2 Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,+ amene amachita chilungamo,+Ndi kulankhula zoona mumtima mwake.+
3 Iye sanena miseche ndi lilime lake.+Sachitira mnzake choipa,+Ndipo satonza bwenzi lake lapamtima.+
4 Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+Koma anthu oopa Yehova amawalemekeza.+Akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.+
5 Sapereka ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+Wochita zinthu zimenezi, sadzagwedezeka konse.+