Salimo 137:1-9

137  Tinakhala pansi+ m’mphepete mwa mitsinje ya ku Babulo,+Ndipo tinalira titakumbukira Ziyoni.+   Tinapachika azeze athu+Pamitengo ya msondodzi.+   Kumeneko, amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+Ndipo otinyozawo anatipempha kuti tiwasangalatse.+ Iwo anati:“Tiimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni.”+   Tingaimbe bwanji nyimbo ya Yehova+M’dziko lachilendo?+   Ndikakuiwala iwe Yerusalemu,+Dzanja langa lamanja liiwale luso lake.   Lilime langa limamatire m’kamwa mwanga+Ngati sindingakukumbukire,+Ngati sindingakweze iwe YerusalemuPamwamba pa chilichonse chimene chimandikondweretsa.+   Inu Yehova, kumbukirani+ zimene ana a Edomu+ ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa,+Iwo anati: “Fafanizani mzindawo! Ufafanizeni mpaka pamaziko ake!”+   Iwe mwana wamkazi wa Babulo, amene udzafunkhidwa,+Wodala ndi amene adzakubwezera+Zimene iwe watichitira.+   Wodala ndi iye amene adzagwira ana ako ndi kuwaphwanya zidutswazidutswa+Mwa kuwawombetsa pathanthwe.

Mawu a M'munsi