Salimo 68:1-35
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo ndi Salimo.
68 Mulungu anyamuke,+ adani ake amwazike,+Ndipo amene amadana naye kwambiri athawe pamaso pake.+
2 Monga mmene mphepo imauluzira utsi, inunso muwauluze chimodzimodzi.+Ngati mmene phula limasungunukira chifukwa cha moto,+Anthu oipa awonongeke ndi kuchotsedwa pamaso pa Mulungu.+
3 Koma olungama asangalale,+Asekerere pamaso pa Mulungu,+Ndipo akondwere ndi kusangalala.+
4 Anthu inu, imbirani Mulungu, muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake.+Muimbireni nyimbo Iye amene akudutsa m’chipululu,+Amene dzina lake ndi Ya,*+ ndipo kondwerani pamaso pake.
5 Tate wa ana amasiye* ndi woweruzira akazi amasiye milandu,+Ndi Mulungu amene amakhala m’malo ake oyera.+
6 Mulungu akuchititsa osungulumwa kukhala m’nyumba.+Akumasula akaidi ndi kuwathandiza kuti zinthu ziwayendere bwino.+Koma anthu osamvera adzakhala m’dziko lowonongeka ndi kutentha kwa dzuwa.+
7 Inu Mulungu, pamene munatsogolera anthu anu,+Pamene munadutsa m’chipululu,+ [Seʹlah.]
8 Dziko lapansi linagwedezeka,+Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,+Phiri ili la Sinai linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu,+ Mulungu wa Isiraeli.+
9 Inu Mulungu, munayamba kugwetsa mvula yamphamvu,+Ngakhale pamene anthu anu anali ofooka, inu munawalimbitsa.+
10 Iwo anakhala mumsasa wanu wa mahema,+Inu Mulungu, chifukwa chakuti ndinu wabwino munakonzera munthu wosautsika msasa wa mahema.+
11 Yehova wapereka lamulo,+Ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.+
12 Mafumu enieniwo okhala ndi magulu a asilikali amathawa, ndithu amathawadi.+Mkazi wongokhala pakhomo, nayenso amagwira nawo ntchito yofunkha.+
13 Ngakhale anthu inu mutagona pakati pa milu ya phulusa mumsasawo,Mudzaona mapiko a njiwa okutidwa ndi siliva,Ndipo nthenga za kumapeto a mapiko ake zidzakhala zagolide wobiriwira monkera ku chikasu.+
14 Pamene Wamphamvuyonse anamwaza mafumu a m’dzikomo,+Mu Zalimoni+ munayamba kugwa chipale chofewa.
15 Dera lamapiri la ku Basana+ ndilo phiri la Mulungu.+Dera lamapiri la ku Basana ndilo phiri la nsonga zitalizitali.+
16 N’chifukwa chiyani inu mapiri a nsonga zitalizitali mumayang’ana mwanjiruPhiri limene Mulungu wafuna kukhalamo?+Yehova adzakhala m’phiri limenelo mpaka muyaya.+
17 Magaleta ankhondo a Mulungu ali m’magulu a masauzande makumimakumi, ali m’magulu a masauzande osawerengeka.+Yehova walowa m’malo oyera kuchokera kuphiri la Sinai.+
18 Mwakwera pamalo apamwamba,+Mwatenga anthu ogwidwa,+Mwatenga mphatso za amuna,+Ndithu inu Yehova* Mulungu, mwatenga ngakhale anthu osamvera,+ kuti inu mukhale pakati pawo.+
19 Adalitsike Yehova, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku,+Mulungu woona wa chipulumutso chathu.+ [Seʹlah.]
20 Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa.+Ndipo njira zopulumukira ku imfa ndi za Yehova,+ Ambuye Wamkulu Koposa.+
21 Ndithudi, Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake kukhala zibenthuzibenthu,+Adzaphwanya liwombo latsitsi la aliyense woyenda m’njira yochimwa.+
22 Yehova wanena kuti: “Ndidzawabweza kuchokera ku Basana,+Ndidzawatulutsa m’nyanja yakuya,+
23 Kuti musambitse mapazi anu m’magazi,+Kuti malilime a agalu anu anyambite magazi a adani anu.”+
24 Iwo aona magulu anu a anthu opambana akuyendera pamodzi, inu Mulungu,+Magulu a anthu oyendera pamodzi a Mulungu wanga, Mfumu yanga, akukalowa kumalo oyera.+
25 Oimba nyimbo anali patsogolo, oimba zoimbira za zingwe anali pambuyo pawo,+Pakati panali atsikana akuimba maseche.+
26 Pamisonkhano tamandani Mulungu,+Tamandani Yehova, inu nonse amene moyo wanu ukuchokera mu Kasupe wa Isiraeli.+
27 Pali fuko laling’ono la Benjamini limene likugonjetsa anthu,+Pali akalonga a Yuda pamodzi ndi makamu awo amene akufuula,Palinso akalonga a Zebuloni ndi akalonga a Nafitali.+
28 Mulungu wanu walamula mphamvu zanu kuti zionekere.+Inu Mulungu, sonyezani mphamvu monga mmene mwachitira kwa ife.+
29 Chifukwa cha kachisi wanu yemwe ali ku Yerusalemu,+Mafumu adzabweretsa mphatso kwa inu.+
30 Dzudzulani nyama yakutchire yokhala m’mabango,+ gulu la ng’ombe zamphongo,+Pamodzi ndi mitundu ya anthu imene ili ngati ana a ng’ombe amphongo, aliyense amene akupondaponda ndalama zasiliva.+Iye wabalalitsa mitundu ya anthu yokonda ndewu.+
31 Zinthu zopangidwa ndi mkuwa wosakaniza ndi zitsulo zina* zidzabwera kuchokera ku Iguputo,+Mwamsanga Kusi adzatambasula dzanja lake ndi kupereka mphatso kwa Mulungu.+
32 Inu maufumu a dziko lapansi, imbirani Mulungu,+Imbani nyimbo zotamanda Yehova [Seʹlah.]
33 Imbirani Iye wokwera kumwamba kwa kumwamba kwakale.+Tamverani! Iye akulankhula ndi mawu amphamvu.+
34 Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu zochuluka.+Iye akulamulira Isiraeli ndipo mphamvu zake zili m’mitambo.+
35 Mulungu akamatuluka m’malo ake opatulika aulemerero, amachititsa mantha.+Iye ndi Mulungu wa Isiraeli, wopereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu.+Mulungu adalitsike.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”
^ Tanthauzo la mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “zinthu zopangidwa ndi mkuwa wosakaniza ndi zitsulo zina” silidziwika. Ena amati tanthauzo lake ndi “akazembe.”