Salimo 98:1-9
Nyimbo.
98 IMBIRANI Yehova nyimbo yatsopano,+Pakuti zimene wachita ndi zodabwitsa.+Dzanja lake lamanja, ndithu mkono wake woyera, wabweretsa chipulumutso.+
2 Yehova wachititsa chipulumutso chake kudziwika.+Chilungamo chake wachisonyeza ku mitundu ya anthu.+
3 Iye wakumbukira lonjezo lake losonyeza kukoma mtima kosatha ndi kukhulupirika kwake ku nyumba ya Isiraeli.+Malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.+
4 Fuulirani Yehova mosangalala chifukwa wapambana, inu nonse anthu a padziko lapansi.+Kondwerani, fuulani mosangalala ndi kuimba nyimbo zomutamanda.+
5 Imbirani Yehova nyimbo zomutamanda ndi zeze,+Muimbireni nyimbo ndi zeze ndi kumutamanda ndi nyimbo zokoma.+
6 Fuulani mwa kuimba malipenga ndi mphalasa.*+Fuulani mosangalala pamaso pa Mfumu Yehova, chifukwa wapambana.
7 Nyanja ndi zonse zili mmenemo zichite mkokomo,+Chimodzimodzinso mtunda ndi zonse zokhala kumeneko.+
8 Mitsinje iwombe m’manja,Mapiri onse afuule pamodzi mokondwera pamaso pa Yehova.+
9 Pakuti iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+Adzaweruza dziko mwachilungamo,+Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu molungama.+
Mawu a M'munsi
^ “Mphalasa” ndi lipenga lopangidwa ndi nyanga ya nkhosa.