Salimo 78:1-72

  • Mulungu ankasamalira Aisiraeli koma iwo analibe chikhulupiriro

    • Mudzauze mʼbadwo wamʼtsogolo (2-8)

    • “Sanakhulupirire Mulungu” (22)

    • “Tirigu wochokera kumwamba” (24)

    • “Ankachititsa kuti Woyera wa Isiraeli amve chisoni” (41)

    • Kuchoka ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa (43-55)

    • ‘Iwo anapitiriza kuyesa Mulungu’ (56)

Masikili.* Salimo la Asafu.+ 78  Inu anthu anga, mvetserani chilamulo changa.*Tcherani khutu ku mawu apakamwa panga.  2  Ndidzatsegula pakamwa panga nʼkunena mwambi. Ndidzanena mawu ophiphiritsa akalekale.+  3  Zinthu zimene tinamva ndipo tikuzidziwa,Zimene makolo athu anatifotokozera,+  4  Sitidzazibisa kwa ana awo.Tidzafotokozera mʼbadwo wamʼtsogolo+Tidzawafotokozera zinthu zotamandika zimene Yehova anachita komanso mphamvu zake,+Zinthu zodabwitsa zimene wachita.+  5  Mulungu anaika chikumbutso pakati pa ana a Yakobo,Ndipo anaika chilamulo mu Isiraeli.Iye analamula makolo athuKuti auze ana awo zinthu zimenezi,+  6  Kuti mʼbadwo wotsatira,Ana amene adzabadwe mʼtsogolo, adzadziwe zimenezi.+ Nawonso adzazifotokoze kwa ana awo.+  7  Zikadzatero anawo azidzadalira Mulungu. Sadzaiwala ntchito za Mulungu+Koma azidzasunga malamulo ake.+  8  Akadzachita zimenezi sadzakhala ngati makolo awo,Mʼbadwo wosamva komanso wopanduka,+Mʼbadwo umene mtima wawo unali wosakhazikika*+Komanso wosakhulupirika kwa Mulungu.  9  Anthu a fuko la Efuraimu anali ndi mauta,Koma anathawa pa tsiku lankhondo. 10  Iwo sanasunge pangano la Mulungu,+Ndipo anakana kutsatira chilamulo chake.+ 11  Iwo anaiwalanso zimene anachita,+Ntchito zake zodabwitsa zimene anawaonetsa.+ 12  Mulungu anachita zodabwitsa pamaso pa makolo awo,+Mʼdziko la Iguputo, mʼdera la Zowani.+ 13  Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,Ndipo anaimitsa madzi nʼkukhala ngati khoma.+ 14  Iye ankawatsogolera ndi mtambo masanaNdipo usiku wonse ankawatsogolera ndi kuwala kwa moto.+ 15  Iye anangʼamba miyala mʼchipululu,Anawalola kumwa madziwo mpaka ludzu kutha ngati kuti akumwa madzi amʼnyanja.+ 16  Iye anatulutsa madzi ochuluka pathanthwe,Ndipo anachititsa madzi ambiri kuti ayende ngati mitsinje.+ 17  Koma iwo anapitiriza kumuchimwiraPopandukira Wamʼmwambamwamba mʼchipululu.+ 18  Iwo anayesa Mulungu mʼmitima yawo+Pomuumiriza kuti awapatse chakudya chimene ankalakalaka. 19  Choncho iwo analankhula mawu amwano kwa MulunguKuti: “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya mʼchipululu muno?”+ 20  Iye anamenya thanthweMoti panatuluka madzi ambiri ndipo mitsinje inasefukira.+ Koma iwo anati: “Kodi angathenso kutipatsa chakudya,Kapena kodi angapatse anthu ake nyama?”+ 21  Yehova atamva zimene ankanenazo anakwiya kwambiri.+Moto+ unayakira Yakobo,Ndipo mkwiyo wake unayakira Isiraeli+ 22  Chifukwa chakuti sanakhulupirire Mulungu.+Sanakhulupirire kuti iye angathe kuwapulumutsa. 23  Choncho Mulungu analamula mitambo yamumlengalenga,Ndipo anatsegula zitseko zakumwamba. 24  Iye anapitiriza kuwagwetsera mana ngati mvula kuti adye.Anawapatsa tirigu wochokera kumwamba.+ 25  Anthu anadya chakudya cha amphamvu.*+Iye anawapatsa chakudya chokwanira.+ 26  Anachititsa kuti mphepo yakumʼmawa iwombe mumlengalenga,Komanso ndi mphamvu zake, anachititsa kuti mphepo yakumʼmwera iwombe.+ 27  Iye anawagwetsera nyama yochuluka ngati fumbi,Anawagwetsera mbalame zochuluka ngati mchenga wamʼmbali mwa nyanja. 28  Anawagwetsera zimenezi mumsasa wawo,Kuzungulira matenti awo onse.* 29  Iwo anadya nʼkukhuta kwambiri.Iye anawapatsa zimene ankalakalaka.+ 30  Koma nkhuli yawo isanathe,Chakudya chawo chidakali mʼkamwa, 31  Mkwiyo wa Mulungu unawayakira.+ Iye anapha amuna amphamvu pakati pawo.+Anapha anyamata a mu Isiraeli. 32  Ngakhale zinali choncho, iwo anapitiriza kumuchimwira,+Ndipo sanakhulupirire ntchito zake zodabwitsa.+ 33  Choncho anathetsa masiku a moyo wawo ngati mpweya,+Ndipo anawabweretsera masoka amene anachititsa kuti afe mwadzidzidzi. 34  Nthawi zonse akayamba kuwapha, iwo ankamufunafuna.+Iwo ankabwerera nʼkuyamba kufunafuna Mulungu, 35  Chifukwa choti ankakumbukira kuti Mulungu anali Thanthwe lawo,+Ndiponso kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba anali Wowawombola.*+ 36  Koma iwo ankafuna kumupusitsa ndi pakamwa pawoKomanso kumunamiza ndi lilime lawo. 37  Mtima wawo sunali wokhulupirika kwa iye.+Ndipo iwo sanali okhulupirika ku pangano lake.+ 38  Koma ankawamvera chifundo.+Ankawakhululukira* machimo awo ndipo sankawawononga.+ Nthawi zambiri ankabweza mkwiyo wake+Mʼmalo moonetsa ukali wake wonse. 39  Iye ankakumbukira kuti iwo ndi anthu athupi la nyama,+Ali ngati mphepo imene imadutsa ndipo sibwereranso.* 40  Nthawi zambiri iwo ankamupandukira mʼchipululu,+Ndipo ankamukhumudwitsa mʼchipululumo!+ 41  Ankayesa Mulungu mobwerezabwereza,+Ndipo ankachititsa kuti Woyera wa Isiraeli amve chisoni.* 42  Iwo sanakumbukire mphamvu za* Mulungu,Tsiku limene anawapulumutsa* kwa mdani wawo,+ 43  Sanakumbukire mmene anasonyezera zizindikiro zake ku Iguputo,+Komanso zinthu zodabwitsa zimene anachita mʼdera la Zowani, 44  Sanakumbukirenso mmene anasandutsira madzi amʼngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo kukhala magazi,+Moti sanathe kumwa madziwo. 45  Mulungu anawatumizira ntchentche zoluma kuti ziwasowetse mtendere,+Komanso achule kuti awawononge.+ 46  Anapereka zokolola zawo kwa dzombe lowononga,Anapereka zipatso za ntchito yawo kwa dzombe lochuluka.+ 47  Anawononga mitengo yawo ya mpesa+Komanso mitengo yawo ya mkuyu ndi matalala. 48  Anapha nyama zawo zonyamula katundu pogwiritsa ntchito matalala,+Ndiponso ziweto zawo ndi mphezi. 49  Anawasonyeza mkwiyo wake woyaka moto,Komanso ukali wake ndipo anawabweretsera mavuto,Anawatumizira magulu a angelo kuti awabweretsere tsoka. 50  Mkwiyo wake anaulambulira njira. Sanawapulumutse ku imfa,Ndipo anawagwetsera mliri.* 51  Pamapeto pake anapha ana onse oyamba kubadwa a ku Iguputo,+Amene ndi chiyambi cha mphamvu zawo zobereka mʼmatenti a Hamu. 52  Kenako anatulutsa anthu ake mʼdzikolo ngati gulu la nkhosa,+Ndipo anawatsogolera mʼchipululu ngati nkhosa. 53  Anawatsogolera ndi kuwateteza,Ndipo sanachite mantha.+Nyanja inamiza adani awo.+ 54  Kenako anawalowetsa mʼdziko lake lopatulika,+Mʼdera lamapiri ili limene dzanja lake lamanja linatenga.+ 55  Iye anathamangitsa mitundu ya anthu kuichotsa pamaso pawo.+Iye anawagawira dzikolo kuti likhale cholowa chawo pochita kuwayezera ndi chingwe.+Anachititsa mafuko a Isiraeli kuti akhale mʼnyumba zawozawo.+ 56  Koma iwo anapitiriza kuyesa Mulungu Wamʼmwambamwamba komanso kumupandukira.+Sanamvere zikumbutso zake.+ 57  Iwo anasiyanso Mulungu ndipo ankachita zinthu mwachinyengo ngati makolo awo.+ Anali osadalirika ngati uta wosakunga kwambiri.+ 58  Anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+Ndipo anamukwiyitsa* ndi zifaniziro zawo zogoba.+ 59  Mulungu anamva ndipo anakwiya kwambiri,+Choncho anawakaniratu Aisiraeli. 60  Pamapeto pake anasiya chihema cha ku Silo,+Tenti imene ankakhalamo pakati pa anthu.+ 61  Analola kuti adani atenge chizindikiro cha mphamvu zake,Analola kuti ulemerero wake ukhale mʼmanja mwa adani.+ 62  Iye anapereka anthu ake ku lupanga,+Ndipo anakwiyira cholowa chake. 63  Moto unapsereza anyamata ake,Ndipo anamwali ake sanawaimbire nyimbo zapaukwati.* 64  Ansembe ake anaphedwa ndi lupanga,+Ndipo akazi awo amasiye sanalire.+ 65  Kenako Yehova anadzuka ngati kuti anali mtulo,+Ngati mmene amadzukira munthu wamphamvu+ pambuyo pomwa vinyo wambiri. 66  Iye anathamangitsa adani ake nʼkuwabweza,+Anachititsa kuti adaniwo akhale onyozeka mpaka kalekale. 67  Iye anakana tenti ya Yosefe,Ndipo sanasankhe fuko la Efuraimu. 68  Koma anasankha fuko la Yuda,+Phiri la Ziyoni limene amalikonda.+ 69  Anachititsa kuti malo ake opatulika akhalepo mpaka kalekale ngati kumwamba,*+Ngati dziko lapansi limene analikhazikitsa mpaka kalekale.+ 70  Anasankha Davide+ mtumiki wake,Ndipo anamuchotsa kumakola a nkhosa,+ 71  Kumene ankaweta nkhosa zoyamwitsa,Anamuika kuti akhale mʼbusa wa ana a Yakobo, omwe ndi anthu ake,+Ndi Isiraeli, amene ndi cholowa chake.+ 72  Iye anawaweta ndi mtima wokhulupirika,+Ndipo anawatsogolera mwaluso.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “malangizo anga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wosakonzeka.”
^ Kapena kuti, “cha angelo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mumsasa wake; mʼmatenti ake.” Kutanthauza a Mulungu kapena a Isiraeli.
^ Kapena kuti, “Wowabwezerera.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ankaphimba.”
^ Kapena kuti, “Moyo wawo umapita ndipo subwereranso.”
^ Kapena kuti, “Ndipo anapweteketsa mtima Woyera wa Isiraeli.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja la.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anawawombola.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anapereka moyo wawo ku mliri.”
^ Kapena kuti, “anamuchititsa nsanje.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo anamwali ake sanatamandidwe.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Anamanga malo ake opatulika ngati malo okwezeka.”