Salimo 17:1-15

  • Pemphero lopempha chitetezo

    • “Mwafufuza mtima wanga” (3)

    • “Mumthunzi wa mapiko anu” (8)

Pemphero la Davide. 17  Imvani dandaulo langa lopempha kuti mundichitire chilungamo, inu Yehova.Mvetserani kulira kwanga kopempha thandizo.Imvani pemphero langa lopanda chinyengo.+  2  Mupereke chigamulo chachilungamo mʼmalo mwa ine.+Maso anu aone kuti ndine wolungama.  3  Mwafufuza mtima wanga, mwandifufuza ngakhale usiku,+Ndipo mwandiyenga.+Mudzapeza kuti ndinalibe zolinga zochita choipa chilichonse.Ndipo pakamwa panga sipanachimwe.  4  Kunena za ntchito za anthu,Mogwirizana ndi mawu apakamwa panu, ndapewa kuyenda mʼnjira za wachifwamba.+  5  Ndithandizeni kuti ndipitirize kuyenda mʼnjira zanu,Kuti mapazi anga asapunthwe.+  6  Ine ndikuitana inu, chifukwa mudzandiyankha,+ inu Mulungu. Tcherani khutu* kwa ine. Imvani mawu anga.+  7  Sonyezani modabwitsa chikondi chanu chokhulupirika,+Inu Mpulumutsi wa anthu amene amathawira kudzanja lanu lamanjaKuthawa anthu amene akupandukirani.  8  Nditetezeni ngati mwana wa diso lanu,+Ndibiseni mumthunzi wa mapiko anu.+  9  Nditetezeni kwa anthu oipa amene akundiukira,Kwa adani* ochokera kufumbi amene andizungulira.+ 10  Mitima yawo siimva chisoni,*Ndipo amalankhula modzikuza ndi pakamwa pawo. 11  Tsopano adaniwo atizungulira,+Akufufuza mpata kuti atigwetse.* 12  Ali ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama,Ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama. 13  Nyamukani, inu Yehova, mulimbane naye+ nʼkumugwetsa.Ndipulumutseni kwa woipayo ndi lupanga lanu. 14  Ndipulumutseni ndi dzanja lanu, inu Yehova,Kwa anthu amʼdzikoli* amene gawo lawo lili mʼmoyo uno,+Anthu amene mwawakhutitsa ndi zinthu zabwino zimene mumapereka+Omwe amasiyira cholowa ana awo aamuna ochuluka. 15  Koma ine ndidzaona nkhope yanu mʼchilungamo.Ndikadzuka ndimadziwa kuti muli nane* ndipo ndimakhutira.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “Weramani ndi kumvetsera.”
^ Kapena kuti, “adani amene akufuna moyo wanga.”
^ Kapena kuti, “Adzikuta ndi mafuta awo omwe.”
^ Kapena kuti, “atiponyere pansi.”
^ Kapena kuti, “amʼnthawi ino.”
^ Kapena kuti, “Ndikadzuka ndimakuonani.”