Salimo 16:1-11

  • Zabwino zonse zimachokera kwa Yehova

    • “Yehova ndi gawo langa” (5)

    • ‘Maganizo amumtima mwanga amandiuza zoyenera kuchita’ (7)

    • ‘Yehova ali kudzanja langa lamanja’ (8)

    • “Simudzandisiya mʼManda” (10)

Mikitamu* ya Davide. 16  Nditetezeni, inu Mulungu, chifukwa ndathawira kwa inu.+  2  Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Yehova. Zinthu zonse zabwino pa moyo wanga zimachokera kwa inu.*  3  Ndipo oyera amene ali padziko lapansi,Anthu aulemerero amenewo, ndi amene amandichititsa kukhala wosangalala kwambiri.”+  4  Anthu amene amafunitsitsa kulambira milungu ina amachulukitsa chisoni chawo.+ Ine sindidzapereka nsembe zachakumwa za magazi kwa milungu ina,Ndipo milomo yanga sidzatchula mayina awo.+  5  Yehova ndi gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa+ komanso kapu yanga.+ Inu mumateteza cholowa changa.  6  Malo amene andiyezera ndi abwino kwambiri. Inde, ndikukhutira ndi cholowa chimene ndapatsidwa.+  7  Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo.+ Ngakhale usiku maganizo amkati mwa mtima wanga* amandiuza zoyenera kuchita.+  8  Ndimaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.+ Chifukwa iye ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.*+  9  Choncho mtima wanga ukusangalala, ndikusangalala kwambiri.* Ndipo ndikukhala motetezeka. 10  Chifukwa simudzandisiya* mʼManda.*+ Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.*+ 11  Mumandidziwitsa njira ya moyo.+ Ndikakhala nanu pafupi,* ndimasangalala kwambiri.+Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe* mpaka kalekale.

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “Ubwino wanga umachokera kwa inu.”
^ Kapena kuti, “mmene ndikumvera mumtima mwanga.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso zanga.”
^ Kapena kuti, “sindidzadzandira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ulemerero wanga ukusangalala.”
^ Kapena kuti, “simudzasiya moyo wanga.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mabaibulo ena amati, “avunde.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndikakhala pafupi ndi nkhope yanu.”
^ Kapena kuti, “chisangalalo.”