Salimo 148:1-14

  • Chilengedwe chonse chitamande Yehova

    • “Mutamandeni, inu angelo ake onse” (2)

    • ‘Mutamandeni, inu dzuwa, mwezi ndi nyenyezi’ (3)

    • Ana komanso achikulire atamande Mulungu (12, 13)

148  Tamandani Ya!* Tamandani Yehova inu okhala kumwamba.+Mutamandeni, inu okhala mʼmwamba.  2  Mutamandeni, inu angelo ake onse.+ Mutamandeni, inu magulu ake onse akumwamba.+  3  Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi. Mutamandeni, inu nyenyezi zonse zowala.+  4  Mutamandeni, inu kumwamba komwe kuli pamwamba kwambiri*Komanso madzi amene ali pamwamba pa kumwamba.  5  Zonsezi zitamande dzina la Yehova,Chifukwa iye analamula ndipo zinalengedwa.+  6  Iye amazichititsa kuti zikhalepo kwamuyaya.+Wapereka lamulo limene silidzatha.+  7  Tamandani Yehova, inu okhala padziko lapansi,Inu zamoyo zikuluzikulu zamʼnyanja komanso inu nonse madzi akuya,  8  Inu mphezi ndi matalala, sinowo* komanso mitambo yakuda kwambiri,Iwe mphepo yamkuntho, amene umakwaniritsa mawu ake,+  9  Inu mapiri ndi inu zitunda zonse,+Inu mitengo ya zipatso ndi inu nonse mitengo ya mkungudza.+ 10  Inu nyama zakutchire+ ndi inu nonse nyama zoweta,Inu zinthu zokwawa ndi mbalame zamapiko. 11  Mutamandeni inu mafumu apadziko lapansi komanso inu nonse mitundu ya anthu,Inu akalonga komanso inu oweruza nonse apadziko lapansi,+ 12  Inu anyamata komanso inu atsikana,*Inu achikulire limodzi ndi ana. 13  Anthu komanso zolengedwa zina zonse, atamande dzina la Yehova,Chifukwa dzina lake lokhalo lili pamwamba poti aliyense sangafikepo.+ Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.+ 14  Iye adzawonjezera mphamvu* za anthu ake,Kuti anthu ake onse okhulupirika atamandike,Amene ndi ana a Isiraeli, anthu amene ali pafupi ndi iye. Tamandani Ya!*

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Mʼchiyankhulo choyambirira, “inu kumwamba kwa kumwamba.”
^ Kapena kuti, “chipale chofewa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anamwali.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakweza nyanga.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.