Salimo 113:1-9

  • Mulungu amene ali kumwamba amadzutsa munthu wonyozeka

    • Dzina la Yehova litamandidwe mpaka kalekale (2)

    • Mulungu amatsika mʼmunsi  (6)

113  Tamandani Ya!* Inu atumiki a Yehova, mutamandeni,Tamandani dzina la Yehova.  2  Dzina la Yehova litamandikeKuyambira panopa mpaka kalekale.+  3  Kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera,Dzina la Yehova litamandidwe.+  4  Yehova ali pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+Ulemerero wake uli pamwamba pa kumwamba.+  5  Ndi ndani angafanane ndi Yehova Mulungu wathu,+Amene amakhala* pamwamba?  6  Iye amatsika mʼmunsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi.+  7  Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa mʼfumbi. Amanyamula munthu wosauka kumuchotsa pamulu wa phulusa*+  8  Kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka,Pamodzi ndi anthu olemekezeka pakati pa anthu a Mulungu.  9  Amachititsa mkazi wosabereka kukhala ndi anaKukhala mayi wosangalala wa ana.*+ Tamandani Ya!*

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Kapena kuti, “Amene wakhala pampando wachifumu.”
^ Mabaibulo ena amati, “kumuchotsa padzala.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ana aamuna.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.