Salimo 110:1-7

  • Mfumu komanso wansembe ngati Melekizedeki

    • ‘Ukalamulire pakati pa adani ako’ (2)

    • Achinyamata odzipereka ali ngati mame (3)

Salimo ndi Nyimbo ya Davide. 110  Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja+Mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”+  2  Yehova adzatambasula ndodo yako yachifumu kuti ulamulirenso madera ena osati mu Ziyoni mokha. Iye adzanena kuti: “Pita pakati pa adani ako ndipo ukawagonjetse.”+  3  Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.* Gulu la achinyamata amene ali ngati mame amʼbandakucha likukuthandiza.Iwo ndi apadera kwa ine komanso ndi okongola.  4  Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo. Iye wati: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,+Mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki!”+  5  Yehova adzakhala kudzanja lako lamanja.+Iye adzaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wake.+  6  Adzapereka chiweruzo ku* mitundu ya anthu.+Adzachititsa kuti mʼdziko mudzaze mitembo ya anthu.+ Adzaphwanya mtsogoleri* wa dziko lalikulu.*  7  Ali mʼnjira, iye* adzamwa madzi amumtsinje. Choncho adzatukula kwambiri mutu wake.

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “pa tsiku limene asilikali ako adzakonzekere kumenya nkhondo.”
^ Kapena kuti, “pakati pa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu.”
^ Kapena kuti, “wa dziko lonse lapansi.”
^ Kutanthauza, “Ambuye wanga” amene atchulidwa mu vesi 1.