Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 78

Yesu Ankalalikira Uthenga wa Ufumu

Yesu Ankalalikira Uthenga wa Ufumu

Yesu atangobatizidwa, anayamba kulalikira kuti: ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ Iye ankalalikira mu Galileya ndi mu Yudeya monse ndipo ophunzira ake ankapita naye limodzi. Yesu atabwerera kwawo ku Nazareti, anapita kusunagoge n’kuyamba kuwerenga mokweza mpukutu wa Yesaya. Iye anati: ‘Yehova wandipatsa mzimu woyera kuti ndilalikire uthenga wabwino.’ Anthu a ku Nazareti ankafuna kuona Yesu akuchita zozizwitsa. Koma zimene anawerengazi zikusonyeza kuti, chifukwa chachikulu chimene Mulungu anam’patsira mzimu woyera, chinali choti azilalikira uthenga wabwino. Kenako Yesu anauza anthuwo kuti: ‘Lero ulosi uwu wakwaniritsidwa.’

Yesu atachoka kumeneku anapita kunyanja ya Galileya komwe anakapeza ophunzira ake 4 akuwedza nsomba. Iye anawauza kuti: ‘Nditsatireni, ndikusandutsani asodzi a anthu.’ Ophunzirawa anali Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane. Nthawi yomweyo iwo anasiya bizinezi yawo yopha nsomba n’kuyamba kumutsatira. Anayenda naye ku Galileya konse n’kumalalikira za Ufumu wa Mulungu. Ankalalikira m’masunagoge, m’misika komanso m’misewu. Kulikonse kumene ankapita anthu ambiri ankawatsatira. Nkhani yokhudza Yesu inali m’kamwam’kamwa moti mpaka inafika ku Siriya.

Yesu anapatsa otsatira ake ena mphamvu zochiritsa komanso kutulutsa ziwanda. Iye ankalalikira m’mizinda komanso m’midzi limodzi ndi ophunzira ake ena. Azimayi angapo okhulupirika ankathandiza Yesu ndi otsatira ake. Ena mwa azimayiwa anali Mariya Mmagadala, Jowana komanso Suzana.

Kenako Yesu anaphunzitsa otsatira akewa n’kuwatumiza kuti akalalikire. Iwo analalikira ku Galileya konse. Anthu ochuluka anakhala ophunzira a Yesu ndipo anabatizidwa. Ambiri ankafuna kuphunzira moti Yesu anawayerekezera ndi m’munda moti mukufunika kukolola. Anati: ‘Pemphani Yehova kuti atumize antchito okakolola.’ Kenako anasankha ophunzira 70 n’kuwatumiza awiriawiri kuti akalalikire ku Yudeya konse. Iwo ankaphunzitsa anthu onse za Ufumu. Ophunzirawa atabwerako, anafotokozera Yesu zinthu zosangalatsa zimene zinachitika. Mdyerekezi sanathe kulepheretsa ntchito yolalikirayi.

Yesu anathandiza ophunzira akewo kuti adzathe kupitiriza ntchito yofunikayi iye akadzapita kumwamba. Anawauzanso kuti: ‘Muzilalikira padziko lonse komanso muziphunzitsa anthu Mawu a Mulungu ndipo muziwabatiza.’

“Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.”​—Luka 4:43