Mawu Ofotokoza Chigawo cha 10
Yehova ndi Mfumu ya chilengedwe chonse. Iye wakhala akulamulira kuyambira kalekale ndipo sadzasiya. Iye anapulumutsa Yeremiya m’chitsime. Anapulumutsanso Sadirake, Mesake ndi Abedinego m’ng’anjo ya moto ndiponso anapulumutsa Danieli m’dzenje la mikango. Iye anatetezanso Esitere n’cholinga choti apulumutse anthu a mtundu wake. Yehova sadzalola kuti zoipa zizingopitirizabe. Ulosi wonena za chifaniziro chachikulu komanso mtengo waukulu umasonyeza kuti Ufumu wa Yehova udzathetsa mavuto onse ndipo udzalamulira dziko lonse.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 57
Yehova Anauza Yeremiya Kuti Azilalikira
Zimene mneneri wachinyamatayu anafotokoza zinakwiyitsa kwambiri akuluakulu a Ayuda.
MUTU 58
Mzinda wa Yerusalemu Unawonongedwa
Ayuda anapitiriza kulambira milungu yonyenga choncho Yehova anawasiya.
MUTU 59
Anyamata 4 Anamvera Yehova
Anyamata achiyuda anakhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale pamene anali kunyumba yachifumu ku Babulo.
MUTU 60
Ufumu Umene Udzalamulire Mpaka Kalekale
Danieli anafotokoza tanthauzo la maloto odabwitsa a Nebukadinezara.
MUTU 61
Anakana Kulambira Fano
Sadirake, Mesake ndi Abedinego anakana kulambira fano la golide la mfumu ya ku Babulo.
MUTU 63
Dzanja Linalemba Pakhoma
Kodi dzanjali linalemba pakhoma pa nthawi iti ndipo zinkatanthauza chiyani?
MUTU 64
Danieli Anaponyedwa M’dzenje la Mikango
Tizipemphera kwa Yehova tsiku lililonse ngati Danieli.
MUTU 65
Esitere Anapulumutsa Anthu a Mtundu Wake
Ngakhale kuti iye anali mlendo m’dzikoli komanso wamasiye anakhala mfumukazi.
MUTU 66
Ezara Ankaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu
Aisiraeli atamvetsera zimene Ezara anawawerengera, anapanga lonjezo lapadera kwa Mulungu.
MUTU 67
Mpanda wa Yerusalemu Unamangidwanso
Nehemiya anamva zoti adani akufuna kuwaukira. N’chifukwa chiyani iye sanaope?