MUTU 91
Yesu Anaukitsidwa
Yesu atafa, munthu wina wachuma dzina lake Yosefe anapita kwa Pilato kukapempha kuti atenge thupi la Yesu n’kukaliika m’manda. Yosefe anapaka thupilo mafuta onunkhira n’kulikulunga munsalu yabwino kwambiri kenako n’kukaliika m’manda ochita kusema. Anagubuduza chimwala ndipo anatseka pakhomo la mandawo. Kenako ansembe aakulu anauza Pilato kuti: ‘Tikuganiza kuti ophunzira a Yesu akhoza kukaba thupi lake n’kumanama kuti wauka.’ Pilato anawayankha kuti: ‘Pitani mukatseke kwambiri mandawo ndipo muikepo alonda.’
Patapita masiku atatu, azimayi ena analawirira kumandako ndipo anapeza kuti chimwala chija chachotsedwapo. M’mandamo munali mngelo ndipo anawauza kuti: ‘Musaope. Yesu wauka. Pitani mukauze ophunzira ake kuti akakumane naye ku Galileya.’
Mariya Mmagadala anathamanga kukauza Petulo ndi Yohane kuti: ‘Thupi la Yesu labedwatu!’ Iwo anapita kumandako n’kukapezadi m’mandamo mulibe thupi la Yesu ndipo anabwerera kwawo.
Mariya atabwerera kumanda kuja anaona angelo awiri ali m’manda ndipo anawafunsa kuti: ‘Kodi Ambuye aja apita nawo kuti?’ Kenako anaona munthu wina ndipo ankaganiza kuti ndi wosamalira munda. Anamuuza kuti: ‘Bambo, ngati ndinu mwawachotsa Ambuye ndiuzeni kumene mwawaika.’ Munthuyo atamuitana kuti: “Mariya!” anazindikira kuti anali Yesu. Choncho anafuula kuti: “Mphunzitsi!” ndipo anamugwira. Yesu anamuuza kuti: ‘Pita ukauze abale anga kuti wandiona.’ Nthawi yomweyo Mariya anapita kukauza ophunzira kuti waona Yesu.
Madzulo a tsiku lomwelo, ophunzira awiri ankayenda kuchoka ku Yerusalemu kupita ku Emau. Ndiyeno munthu wina anayamba kuyenda nawo ndipo anawafunsa zimene ankakambirana. Iwo anati: ‘Kodi iwe sunamve? Masiku atatu apitawa ansembe aakulu anapha Yesu. Ndiye panopa azimayi ena akunena kuti ali moyo.’ Munthuyo anawafunsa kuti: ‘Kodi inu simukhulupirira zimene aneneri ananena? Pajatu anati Khristu adzafa kenako adzaukitsidwa.’ Munthuyo anawafotokozera malemba
osiyanasiyana. Atafika ku Emau, ophunzirawo anamupempha kuti apite nawo kwawo. Pa nthawi ya chakudya chamadzulo, munthuyo anapemphera ndipo anamuzindikira kuti anali Yesu. Kenako anasowa.Nthawi yomweyo ophunzirawo anapita ku Yerusalemu ndipo anakalowa m’nyumba yomwe munali atumwi. Kumeneko anawafotokozera zomwe zinachitika. Ali m’nyumbamo, Yesu anatulukira. Poyamba, atumwiwo sanakhulupirire kuti ndi Yesu. Koma iye anawauza kuti: ‘Onani manja angawa, ndigwireni kuti mutsimikize. Paja Malemba ananeneratu kuti Khristu adzaukitsidwa.’
“Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”—Yohane 14:6