Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 8

Abulahamu ndi Sara Anamvera Mulungu

Abulahamu ndi Sara Anamvera Mulungu

Pafupi ndi mzinda wa Babele panali mzinda wina wotchedwa Uri. Anthu a mumzinda umenewu ankalambira milungu ina osati Yehova. Koma mumzindawu munali munthu wina amene ankalambira Yehova yekha. Dzina lake anali Abulahamu.

Tsiku lina Yehova anauza Abulahamu kuti: ‘Samuka mumzindawu ndipo upite kudziko limene ndidzakuuze.’ Apa ndiye kuti Abulahamu anafunika kusiya nyumba yake ndi abale ake. Kenako Mulungu anamuuza kuti: ‘Ndidzapangitsa kuti ukhale mtundu waukulu. Ndipo kudzera mwa iweyo ndidzadalitsa anthu onse a padziko lapansi.’

Abulahamu sankadziwa kumene Yehova akufuna kuti apite, koma ankakhulupirira kwambiri Yehovayo. Choncho iye ndi mkazi wake, Sara analongedza katundu n’kuyamba ulendo wautali. Pa ulendowu ananyamukanso ndi bambo ake, dzina lawo a Tera komanso Loti yemwe anali mwana wa mng’ono wake.

Pa nthawiyi n’kuti Abulahamu ali ndi zaka 75. Ndipo iye ndi banja lake atayenda kwa nthawi yaitali, anafika m’dziko limene Yehova anawauza. Dziko lake linali la Kanani. Ali kumeneko, Mulungu analankhula ndi Abulahamu n’kumulonjeza kuti: ‘Dziko lonseli ndidzalipereka kwa ana ako.’ Komatu pa nthawiyi Abulahamu ndi Sara n’kuti ali okalamba ndipo analibe ana. Ndiye kodi Yehova akanakwaniritsa bwanji lonjezo lakeli?

“Mwa chikhulupiriro, Abulahamu . . . anamvera ndi kupita kumalo amene anali kuyembekezera kuwalandira monga cholowa. Iye anapitadi, ngakhale sanadziwe kumene anali kupita.”​—Aheberi 11:8