MUTU 88
Yesu Anamangidwa
Yesu ndi atumwi ake anadutsa m’chigwa cha Kidironi n’kupita kuphiri la Maolivi. Apa n’kuti nthawi itapitirira 12 kokolo ya usiku ndipo mwezi unali wathunthu. Atafika m’munda wa Getsemane Yesu anauza atumwiwo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.” Kenako anapita chapatali ndipo anagwada n’kuyamba kupemphera. Iye anali ndi nkhawa kwambiri ndipo anapemphera kwa Yehova kuti: “Chifuniro chanu chichitike.” Yehova anatumiza mngelo kuti adzalimbikitse Yesu. Atapita pamene panali atumwi paja, anapeza atumwi atatu akugona. Iye anawauza kuti: ‘Dzukani! Ino si nthawi yogona. Nthawi yafika yoti ndiperekedwe kwa adani.’
Pasanapite nthawi Yudasi anatulukira ali ndi gulu la anthu onyamula malupanga ndi zibonga. Yesu ndi atumwi ake ankakonda kupita kumunda wa Getsemani. Choncho Yudasi ankadziwa kuti Yesu angapezeke kumeneku. Iye anali atauza anthuwo kuti akachita zinazake kuti iwo akathe kuzindikira Yesu. Choncho anangofikira pamene panali Yesu n’kunena kuti: ‘Muli bwanji Mphunzitsi?’ Kenako anamupsompsona. Koma Yesu anati: ‘Yudasi, kodi ukundipereka pondipsompsona?’
Yesu anayandikira gululo n’kulifunsa kuti: “Mukufuna ndani?” Anthuwo anayankha kuti: ‘Yesu wa ku Nazareti.’ Ndiyeno iye anayankha kuti: “Ndine.” Koma anthuwo anabwerera m’mbuyo n’kugwa pansi. Yesu anawafunsanso kuti: ‘Ndati mukufuna ndani?’ Iwo anayankhanso kuti: ‘Yesu wa ku Nazareti.’ Yesu anawauza kuti: ‘Ndakuuzani kuti, ndine. Asiyeni awa azipita.’
Nthawi yomweyo Petulo anasolola lupanga lake n’kudula khutu la Makasi, yemwe anali wantchito wa mkulu wa ansembe. Koma Yesu anatenga khutulo n’kuliika pamalo ake ndipo anamuchiritsa. Kenako anauza Petulo kuti: ‘Bwezera lupangalo pamalo ake. Ukamapha anthu ndi lunganga, nawenso udzaphedwa ndi lupanga.’ Asilikaliwo anagwira Yesu n’kumumanga ndipo atumwi aja anathawa. Kenako asilikaliwo anatenga Yesu n’kupita naye
kwa wansembe wamkulu, dzina lake Anasi. Atamufunsa mafunso anamutumiza kwa mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa. Koma kodi atumwi aja zinawathera bwanji?“M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”—Yohane 16:33