Mawu Ofotokoza Chigawo 2
N’chifukwa chiyani Yehova anabweretsa chigumula chimene chinawononga zamoyo zonse? Kale kwambiri anthu asanachuluke padzikoli, panachitika nkhani inayake. Nkhaniyi inachititsa kuti munthu aliyense azifunika kusankha kuchita zabwino kapena zoipa. Anthu ena monga Adamu, Hava ndi mwana wawo Kaini anasankha kuchita zoipa. Koma panalinso anthu ena ochepa monga Abele ndi Nowa omwe anasankha kuchita zabwino. Pofika nthawi ya Nowa anthu ambiri ankachita zoipa n’chifukwa chake Yehova anawononga dziko loipalo. Chigawochi chitithandiza kudziwa kuti Yehova amaona zimene timasankha ndipo sadzalola kuti choipa chigonjetse chabwino.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 3
Adamu ndi Hava Sanamvere Mulungu
M’munda wa Edeni, kodi mtengo umodzi unali wosiyana bwanji ndi mitengo ina? N’chifukwa chiyani Hava anadya zipatso za mtengowo?
MUTU 4
Anakwiya Mpaka Anapha M’bale Wake
Mulungu analandira nsembe ya Abele koma ya Kaini anaikana. Kaini ataona zimenezi, anakwiya kwambiri ndipo anapha Abele.
MUTU 5
Chingalawa cha Nowa
Angelo oipa atakwatira akazi padzikoli anabereka ana amene ankavutitsa anthu. Chiwawa chinali ponseponse. Koma Nowa sankachita nawo zoipa. Iye ankakonda Mulungu komanso ankamumvera.
MUTU 6
Anthu 8 Anapulumuka
Yehova anabweretsa chigumula pogwetsa mvula kwa masiku 40, usana ndi usiku. Nowa ndi banja lake anakhala m’chingalawa kwa nthawi yoposa chaka. Kenako Mulungu anawauza kuti atuluke.