MUTU 4
Anakwiya Mpaka Anapha M’bale Wake
Adamu ndi Hava atathamangitsidwa m’munda wa Edeni, anakhala ndi ana ambiri. Mwana wawo woyamba anali Kaini ndipo wachiwiri anali Abele. Kaini anali mlimi koma Abele anali m’busa.
Tsiku lina, Kaini ndi Abele anapereka nsembe kwa Yehova. Kodi ukudziwa kuti nsembe ndi chiyani? Ndi mphatso yapadera. Yehova anasangalala ndi nsembe ya Abele koma sanasangalale ndi ya Kaini. Ndiyeno Kaini anakwiya kwambiri. Yehova anamulangiza kuti asiye kukwiya chifukwa akhoza kuchita zoipa. Koma Kaini sanamvere.
Ndiyeno Kainiyo anauza Abele kuti: ‘Tiye tipite kumunda.’ Ali kumundako, anayamba kumenya m’bale wakeyo mpaka kumupha. Kodi Yehova anatani?
Analanga Kaini pomuthamangitsira kutali ndipo sanamulole kuti abwererenso kwawo.Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Nthawi zina tingakhumudwe zinthu zikakhala kuti sizinayende mmene timafunira. Koma tikaona kuti tayamba kukwiya kwambiri kapena ena akatilangiza, tiyenera kusiya kukwiyako, kuopera kuti tingayambe kuchita zosayenera.
Popeza Abele ankakonda Yehova komanso ankachita zabwino, Yehova sadzamuiwala. Adzamuukitsa kuti adzakhale m’paradaiso.
“Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.”—Mateyu 5:24