Pitani ku nkhani yake

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni limene linakhazikitsidwa ndi Yehova Mulungu. M’Baibulo, “Ufumu wa Mulungu” umatchedwanso “ufumu wakumwamba” chifukwa likulu lake lili kumwamba. (Maliko 1:14, 15; Mateyu 4:17) Ngakhale kuti Ufumuwu uli ndi mbali zambiri zofanana ndi maboma a masiku anowa, koma ndi wapamwamba kwambiri kuposa boma lililonse.

  • Olamulira ake: Mulungu anasankha Yesu Khristu kukhala Mfumu ya Ufumuwu ndipo anamupatsa mphamvu zoposa wolamulira aliyense. (Mateyu 28:18) Yesu amagwiritsira ntchito bwino mphamvuzi ndipo ali padziko lapansi anasonyeza kale kuti ndi wolamulira wodalirika komanso wachifundo. (Mateyu 4:23; Maliko 1:40, 41; 6:31-34; Luka 7:11-17) Motsogoleredwa ndi Mulungu, Yesu wasankha anthu ochokera m’mitundu yonse omwe “adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi” limodzi ndi Yesuyo ali kumwamba.—Chivumbulutso 5:9, 10.

  • Kutalika kwa nthawi imene Ufumuwu udzalamulire: Mosiyana ndi maboma a anthu, omwe amalamulira kenako n’kuchoka, Ufumu wa Mulungu “sudzawonongedwa ku nthawi zonse.”—Danieli 2:44.

  • Nzika za Ufumu: Aliyense amene amachita zinthu zimene Mulungu amafuna adzakhala nzika ya Ufumu wa Mulungu, mosatengera mtundu kapena kumene anabadwira.—Machitidwe 10:34, 35.

  • Malamulo: Malamulo a Ufumu wa Mulungu sikuti amangoletsa nzika zake kukhala ndi khalidwe loipa. M’malomwake, nzika za Ufumuwu zimaphunzitsidwanso kukhala ndi makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, Baibulo limati: ‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ (Mateyu 22:37-39) Anthu omwe ndi nzika za Ufumuwu amakonda Mulungu ndiponso anzawo, ndipo zimenezi zimawachititsa kuti azichitira ena zabwino.

  • Zimene Ufumuwu umaphunzitsa: Yehova Mulungu anapereka mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino kwa anthu omwe ndi nzika za Ufumu wake, ndiponso amawaphunzitsa mmene angatsatirire mfundozo.—Yesaya 48:17, 18.

  • Cholinga cha Ufumuwu: Olamulira a Ufumu wa Mulungu sikuti amadyera masuku pamutu anthu omwe ndi nzika za Ufumuwu. M’malomwake, iwo amachita zinthu n’cholinga choti Mulungu akwaniritse malonjezo ake, monga lonjezo lakuti anthu amene amamukonda adzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi.—Yesaya 35:1, 5, 6; Mateyu 6:10; Chivumbulutso 21:1-4