MUTU 82
Yesu Anaphunzitsa Otsatira Ake Kupemphera
Afarisi ankakonda kuchita zinthu n’cholinga chongofuna kugometsa anthu. Akachitira munthu zabwino, ankafuna kuti aliyense adziwe. Ankakonda kupemphera pamene pamadutsa anthu ambiri kuti anthuwo aziwaona. Komanso iwo ankaloweza mapemphero n’kumawanena m’masunagoge kapena pamphambano n’cholinga choti anthu azimva. Choncho anthu anadabwa pamene Yesu anawauza kuti: ‘Musamapemphere ngati Afarisi. Iwo amaganiza kuti Mulungu angachite chidwi ndi mapemphero awo aatali. Pemphero ndi nkhani ya pakati pa Yehova ndi munthu amene akupempherayo. Ndiponso musamabwereze zomwezomwezo popemphera. Mulungu amafuna kuti muzimuuza zimene zili mumtima mwanu, osati zongoloweza.’
Yesu ananenanso kuti: ‘Popemphera muzinena kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere.
Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.”’ Anawauzanso kuti angathe kupempha chakudya cha tsikulo. Komanso angapemphe kuti Mulungu awakhululukire machimo awo ndiponso kuti awathandize pa zinthu zina zokhudza iwowo.Yesu anati: ‘Musasiye kupemphera. Pitirizani kupempha Atate wanu Yehova kuti akupatseni zinthu zabwino. Makolo amapatsa ana awo zinthu zabwino. Mwana wanu atakupemphani chakudya simungamupatse mwala. Komanso atakupemphani nsomba simungamupatse njoka.’
Kenako anati: ‘Ngati inu mumapatsa ana anu zinthu zabwino, ndiye kuli bwanji Atate wanu Yehova? Iye adzakupatsani mzimu woyera. Chofunika ndi kumupempha basi.’ Kodi iweyo umatsatira malangizo a Yesuwa? Kodi ukamapemphera umatchula zinthu ziti?
“Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.”—Mateyu 7:7