MUTU 38
Yehova Anapatsa Mphamvu Samisoni
Pa nthawi ina, Aisiraeli anayambanso kulambira mafano ndipo Yehova analola Afilisiti kuti aziwalamulira mwankhanza. Koma panali Aisiraeli ena amene ankakondabe Yehova. Chitsanzo ndi munthu wina dzina lake Manowa. Koma iye ndi mkazi wake analibe ana. Ndiyeno tsiku lina, Yehova anatuma mngelo kuti apite kwa mkazi wa Manowa. Mngeloyo anauza mkaziyo kuti: ‘Udzakhala ndi mwana wamwamuna amene adzapulumutse Aisiraeli kwa Afilisiti. Koma mwanayo adzakhala Mnaziri.’ Kodi iwe Anaziri umawadziwa? Anaziri anali atumiki apadera a Yehova ndipo sankaloledwa kumeta tsitsi.
Patapita nthawi, mkazi wa Manowa anakhaladi ndi mwana ndipo anamupatsa dzina loti Samisoni. Mwanayo atakula, Yehova anamupatsa mphamvu zambiri. Iye anapha mkango popanda chida chilichonse. Tsiku lina ali yekha anapha Afilisiti 30. Afilisiti ankadana kwambiri ndi Samisoni ndipo ankafufuza njira yoti amuphere. Tsiku lina iye akugona ku Gaza, Afilisiti anapita pageti la mzindawo n’kumamudikirira kuti amuphe kukacha. Koma Samisoni anadzuka pakati pa usiku n’kuzula getilo. Iye analinyamula mpaka kukalitaya paphiri linalake la pafupi ndi ku Heburoni.
Zitatero, Afilisiti anapita kwa chibwenzi cha Samisoni dzina lake Delila. Iwo anamuuza kuti: ‘Iwe, kodi chinsinsi cha mphamvu za Samisoni chili pati? Ukatiuza tikupatsa ndalama zambiri. Tikufuna timugwire n’kumutsekera m’ndende.’ Delila anali wokonda ndalama moti anawauza kuti afufuza. Poyamba Samisoni ankakana kufotokozera Delila chinsinsicho. Koma iye anakakamira kwambiri moti Samisoni anafika potopa nazo ndipo anamuululira. Iye anati: ‘Ine ndine Mnaziri. Sindinametepo tsitsi langali. Kungondimeta, mphamvu zanga zonse zithera pomwepo.’ Samisoni akanadziwa sakanaulula zimenezi.
Nthawi yomweyo Delila anauza Afilisiti kuti: ‘Wandiuza chinsinsi chake chija.’ Kenako anamugoneka Samisoni pa miyendo n’kuitana munthu woti
amumete. Atamumeta, Delila uja anafuula kuti: ‘Samisoni! Afilisititu abwera.’ Samisoni anadzuka koma alibiretu mphamvu. Afilisitiwo anamugwira n’kumuchotsa maso kenako anakamutsekera m’ndende.Tsiku lina, Afilisiti anasonkhana mukachisi amene ankalambiramo mulungu wawo dzina lake Dagoni. Iwo ankafuula kuti: ‘Mulungu wathu watipatsa Samisoni. Mtulutseni tisewere naye.’ Ndiyeno anthuwo anamuimika pakati pa zipilala ziwiri n’kumamuseka. Koma Samisoni anafuula kuti: ‘Yehova, chonde ndipatseni mphamvu kamodzi kokhaka.’ Pa nthawiyi tsitsi lake linali litamereranso. Iye anakankha zipilalazo ndi mphamvu zake zonse. Chinyumba chonsecho chinagwa ndipo chinapha anthu onse. Nayenso Samisoni anafera momwemo.
“Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13