MUTU 87
Chakudya Chamadzulo Chomaliza
Ayuda ankachita chikondwerero cha Pasika pa tsiku la 14 la mwezi wa Nisani. Ankachita izi pokumbukira zimene Mulungu anachita powapulumutsa ku Iguputo kuti akakhale m’Dziko Lolonjezedwa. Mu 33 C.E., Yesu ndi atumwi ake anachita mwambowu ku Yerusalemu m’chipinda chapamwamba. Pomaliza, Yesu ananena kuti: ‘Mmodzi wa inu adzandipereka.’ Atumwiwo anadabwa kwambiri ndipo anafunsa Yesu kuti: ‘Mukunena ndani?’ Yesu anayankha kuti: ‘Amene ndimupatse mkatewu.’ Kenako anapereka mkate kwa Yudasi Isikariyoti. Nthawi yomweyo Yudasi anatuluka.
Yesu anapemphera ndipo kenako ananyemanyema mkate n’kupereka kwa atumwiwo. Ndipo anati: ‘Idyani mkatewu. Ukuimira thupi langa limene ndidzapereke chifukwa cha inu.’ Kenako anapempheranso n’kupereka vinyo kwa atumwiwo. Ananena kuti: ‘Imwani vinyoyu. Akuimira magazi anga amene ndidzapereke n’cholinga choti machimo a anthu akhululukidwe. Muzichita zimenezi chaka chilichonse pondikumbukira. Ndikukulonjezani kuti tidzakalamulira limodzi kumwamba.’ Kuyambira nthawi imeneyo, otsatira a Khristu amachita mwambo wokumbukira imfa yake chaka chilichonse. Mwambo umenewu umatchedwa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.
Atangomaliza mwambowu, atumwiwo anayamba kukangana. Nkhani yake inali yoti wamkulu ndani. Koma Yesu anawauza kuti: ‘Wamkulu kwambiri pa nonsenu, ndi amene amadziona kuti ndi wamng’ono kwambiri.
‘Inutu ndinu anzanga. Ndimakuuzani chilichonse chimene Atate wanga wafuna kuti ndikuuzeni. Posachedwapa ndipita kumwamba kwa Atate. Anthu adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mumakondana. Choncho muzikondana ngati mmene ine ndimakukonderani.’
Pomaliza, Yesu anapempha Yehova kuti ateteze ophunzira ake. Anapemphanso kuti awathandize kuti azichita zinthu mogwirizana komanso mwamtendere. Kenako anapempha kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. Ndiyeno Yesu ndi atumwiwo anaimba nyimbo zotamanda Yehova kenako anatuluka m’chipindamo. Apa tsopano nthawi yoti Yesu amangidwe inali itayandikira.
“Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.”—Luka 12:32